Bwalo la milandu ku Zomba layamba kumva mulandu wa a Bon Kalindo

Advertisement
Bon Kalindo Malawi

Bwalo la Principal Resident’s Magistrate ku Zomba layamba kumva mulandu wa mkulu wa Bungwe la Malawi First a Bon Kalindo omwe akuwaganizira kuti adayambitsa chisokonezo pa ziwonetsero zomwe adachititsa mu Mzinda wa Zomba pa 23 November chaka chatha.

Apolisi atsekulira mulandu a Bon Kalindo powaganizira kuti adayambitsa chisokonezo panthawi yomwe adachititsa ziwonetsero mu mwezi wa November chaka chatha koma a Kalindo awukana mulanduwo.

Wapolisi oyimira Boma pamilandu mchigawo chakum’mawa Senior Superintendent Josephine Chigawa adawuza bwalo kuti mbali ya Boma ili ndi mboni zisanu ndi ziwiri (7) ndipo mboni zitatu zaperekera kale umboni pomwe mulanduwu udayamba.

Poyankhulapo, loya yemwe akuyimilira a Kalindo pa mulanduwu Timothy Chirwa adati ndiwokhutira ndi momwe mlanduwu  wayambira ndipo adati pakali pano sangayankhule zambiri momwe mboni zambali ya Boma zaperekera umboni wao.

Yemwe akuzenga mulanduwu Principal Residents Magistrate Martin Chipofya wayamba kaye wayimitsa mulanduwu mpaka pa 30 January pomwe mbali ya Boma ikuyembekezeka kudzabweretsa mboni zina zinai kuti zizapitilidze kuperekera umboni.

Advertisement