Tidzalemekeza voti ya aliyense – chatero chipani cha EFP


Vice president of a new political party in Malawi

A Griffin Maruwasa, omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha ndale chomwe chikhadzikitsidwe posachedwapa cha Economic Freedom Party (EFP) atsindika kuti chipani chawo chidzawonetsetsa kuti voti ya anthu ikulemekezedwa.

A Maruwasa anena izi poyankhulana ndi Malawi24 pakutha pa mkumano omwe adali nawo ndi mamembala a chipanichi m’boma la  Balaka.

Iwo adati kwa nthawi yaitaili, zipani za ndale mdziko muno zakhala zikulonjeza malonjezo ambiri pa misonkhano yokopa anthu ngakhale ati zipanizi zikalowa m’boma sizikwanilitsa mkomwe mfundo za mu malonjezo awo.

“Kuyambira mu chaka cha 1994, zipani zandale zosiyanasiyana zakhala zikubweletsa mfundo zawo zokopa anthu. Komabe, atsogoleri ake amaiwala malonjezo awo mu nthawi yokopa anthu akangolowa m’boma. Uku ndi kulakwa kwambiri chifukwa zimasonyeza kusalabadira komanso kusalemekeza voti ya anthu” adafotokoza Maruwasa.

A Maruwasa adawonjezeranso  kunena kuti chipani chawo sichili pa changu kulowa m’boma posachedwapa koma anenetsa kuti iwo ali okonzeka kugwira ntchito ndi chipani chandale chilichonse chomwe chidzawonetse chidwi komanso kuthekera kovomeleza mfundo zomwe chipani cha EFP chizakhadzikitse.

Malingana ndi a Maruwasa, chipani chawo chidzawonetsetsa kuti chikuika mfundo zokomera onse makamaka achinyamata, amai komanso okalamba omwe azalimbikitsidwe komanso kupatsidwa danga lotukula dziko lino kudzera mu ntchito zachitukuko zosiyanasiyana.

A Maruwasa adatinso Padakali pano, zonse zokonzekera kukhadzikitsa chipanichi zili mchimake.

One comment on “Tidzalemekeza voti ya aliyense – chatero chipani cha EFP

Comments are closed.