Kuchepa kwa malipiro kukukolezera mchitidwe okuba mu ma kampani a amwenye

Advertisement

Ogwira ntchito mu ma kampani a amwenye mu mzinda wa Blantyre akuti akukakamikizika kuyamba mchitidwe ozembetsa katundu m’malo ogwirira ntchito ndi kumakagulitsa chifukwa cha kuchepa kwa malipiro.

M’modzi mwa ogwira ntchito wina yemwe anati tisamutchule dzina anati ndalama yomwe amalandira imakhala yochepa zomwe zimakhala zovuta kusamalira mabanja awo ndipo zimayambitsa anthu ogwira ntchito kukhala ndi maganizo omazembetsa katundu ngati njira imodzi yothana ndi mavuto a zachuma.

“Sichimakhala cholinga kuti tibe koma vuto limakhala loti tikulandira ndalama yochepa ndiye munthu umafunika uzizilipira wekha. Kupanda kutero ndiye kuti ukhala kapolo,” anatero mnyamatayo.

M’modzi wa anthu omwe amagwira ntchito ku kampani yokonza zakumwa ya Sun Crest nayenso anadandaula kuti pa tsiku amalandira K2000 ndipo ndalama imeneyi ndi imene amakagulira chakudya komaso kulipira nyumba yomwe ndimakhala ndi banja lake.

“Tsiku ndi tsiku ndimasiya K3000 kuti agule zakudya ndipo nyumba yomwe timakhala ndi ya K25,000 koma ndalama yomwe timalandira siposera K50,000 kamba koti masiku ena sitipita kukagwira ntchito.

“Ntchito yomwe timagwira ndi yochuluka ndipo nthawi zina timaweruka mochedwa koma kuwadandulira za malipiro anthu kuti atikwezele satiyankha kathu.” anatero bambowo.

Mayi wina yemwe amagwira ganyu ku kampani yokonza mafuta ophikira ya Oil Refined Campany anapempa boma komaso ma bungwe kuti alowererepo pa nkhani yokweza malipiro.

Iyeyu anadandaula motere: “Moyo ukuvuta kwambiri kamba koti tsiku lililonse ndalama yomwe ndimapeza ndikagwira ganyu siposera K1,500 ndipo ndimalephera kugula zofunikira pa moyo wanga.”

Boma kudzera mu unduna owona za anthu apa ntchito linakhazikitsa malipiro oyambira osachepera K100,000 kwa  aliyese yemwe akugwira ntchito posatengera malo omwe akugwira ntchito.

Bungwe loyang’anira anthu apa ntchito la Malawi Congress of Trade Unions (MCTU) limalimbikitsa boma kuti tichite machawi popanga kafukufuku ngati ogwira ntchito ambriri akulandiradi malipiro atsopanowa.

Advertisement