Msewu wa Lakeshore waduka

Advertisement
Lakeshore road has been cut off in Salima

Tsopano mayendedwe akhala wovutirapo pa msewu wa M5 pamene madzi ochuluka adula msewuwu, omwe umatchedwanso kuti Lakeshore, kamba ka mvula yamphamvu yomwe yakhala ikugwa.

Msewu umenewu waduka pa malo otchedwa Mwalawoyera kuchokera pa Salima Turn Off kupita ku Salima.

Malingana ndi a Portia Kajanga omwe ndi ofalitsa nkhani za bungwe la Roads Authority, izi zili chomwechi kamba kakuti anthu ena akhala akuba zitsulo zapa mlathowo.

Iwo atsimikiza kuti pakadali pano palibe galimoto yomwe ingadutse pamalopo kamba kakuti mlathowo waonongekeratu.

A Kajanga apempha anthu kuti ngati akufuna kuti agwiritse ntchito msewu umenewu akuyenera kudzera msewu wa Khwekhwelele (Golomoti) ngati akufuna kupita ku Salima pamene akuchokera ku Ntcheu kapena ku Balaka.

Iwo afotokozanso kuti akatswiri owona za msewu afika kale pamalopo kukonza mlathowu pofuna kuti ntchito zamayendedwezi zibwelele m’chimake.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement