M’mimba ndi nchipala: Apolisi m’boma la Mangochi akusakasaka mnyamata wina wa zaka 15 yemwe akuti wabaya pakhosi ndikupha mchemwali wake wa zaka 25 ati kamba koti amamukaniza kukazingira chimanga mu poto watsopano.
Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mangochi a Amina Tepani Daudi omwe azindikira malemuwa ngati a Fyness Chapweteka omwe akumana ndi tsokali Lachinayi pa 11 January, 2024 ku mudzi kwawo kwa Mtendere, mdera la mfumu yaikulu Chilipa m’bomalo.
A Tepani Daudi ati mayi wa anawa awuza apolisi kuti patsikuli mnyamatayo adatenga poto watsopano yemwe malemu Chapweteka adagula kuti adziphikila zinthu zosiyanasiyana pakhomopo ndikumakazingilamo chimanga.
Malemu Chapweteka omwe anagula potoyu ataona izi anakwiya kwambiri ndipo adamuuza mchimwene wawoyo kuti potoyo siokazingila chimanga koma kuphikira zakudya zina ndipo pamapeto pake mkangano pakati pa awiriwa udabuka.
Nkanganowu utafika pa mwana wakana phala, awiriwa anayamba kumenyana ndipo kenaka mnyamatayo adatenga mpeni ndikubaya Chapweteka pakhosi ndipo poti nkhuyu zodya mwana zipota akulu, mayi wa anawa anathamangira ndi Chapweteka kuchipatala cha Phirilongwe m’bomalo.
Atafika naye ku chipatala, madotolo anauzaso khololo kuti Chapweteka adali atamwalira kale pomwe amafika naye ndipo zotsatira za chipatala zaonetsa kuti imfa ya Chapweteka idachitika kamba koti adataya magazi ochuluka.
Pakali pano mnyamatayo sakudziwika komwe ali ndipo apolisi akhazikitsa kafukufuku omusaka kuti akayankhe mlandu wakupha.