Mkangano wa malire a Malawi ndi Mozambique wavuta ku Mangochi

Advertisement
Malawi Mozambique border at Makanjira

Adindo awapempha kuchita machawi kuthetsa kusamvana pankhani ya malire a dziko lino ndi dziko la Mozambique ku Mangochi pomwe akuti apolisi ndi anthu a m’dziko la Mozambique atchetcha chimanga cha a Malawi ku midzi ina kudera la mfumu yaikulu Makanjira m’bomalo ponena kuti malowo ali m’dziko lawo la Mozambique.

Malingana ndi zomwe tsamba lino lapeza, kusamvanaku kunayamba zaka zapitazo pomwe boma la Malawi linachita mgwirizano ndi boma la Mozambique pa ntchito yofuna kuwunikaso malire a mayiko awiriwa omwe poyamba anagawidwa mchaka cha 1920 ndipo ntchito yowunikaso malirewa inayambika mu chaka cha 2012.

Munthu amene watitsina khutu za nkhaniyi yemwe anasankha kusatchulidwa mu nkhani ino, wati panachitika chinyengo chachikulu pa nthawi yowunikaso malirewa kamba koti akuluakulu a dziko la Mozambique analowa mkati mwa dziko la Malawi ndikuika zizindikira za malire (boundary beacons).

Munthuyu watiuza kuti mafumu komaso anthu akudelari atafusa za tanthauzo la zomwe zinaikidwazo nthawi imeneyo, anayankhidwa ndi akuluakulu a mdziko la Mozambique kuti zimenezo si malire koma manetiweki (network) chabe omwe akugwilitsidwa ntchito pa ntchito yowunikaso malireyo koma akuti ntchitoyi itatha anadabwa kuti pa ma mabikoni aja analembapo mawu osonyeza kuti amenewo ndiye malire atsopano a dziko la Malawi ndi Mozambique.

Tauzidwaso kuti mu chaka cha 2016 nkhaniyi inafika povuta kwambiri pomwe apolisi a Malawi anachoka kuderako ndikusiya kopanda chitetezo, ndipo chipata chakumeneku (border) chinatsekedwa mpaka pano koma anangosiya ku Roadblock yokha yomweso akuti ili patali ndi anthu.

Chatsitsa dzaye ndichakuti apolisi komanso anthu wamba a m’dziko la Mozambique kumayambiliro kwa mwezi wa December, 2023 anapita kumidzi yomwe a Malawi anadzalako chimanga ndikuchitchetcha ponena kuti malo omwe akhala akulima kwa zaka zambiriwo, ali mdziko lawo la Mozambique.

Zikumvekaso kuti anthu ndi apolisi a mdziko la Mozambique-wa apanga izi kamba kokhumudwa kuti ina mwa midzi yomwe iwo amaitenga kuti ili mdziko lawo, boma la Malawi laikako mapolo (pole) a magetsi.

“Pano nkhani yafika povuta kamba koti kumaloko kwaikidwa mapolo a dziko la malawi ndi pameneno anthu aku Mozambique abwera ndikumawazunza anthu kumati bwanji aika mapolo a magetsi mu dziko la Mozambique. Ndikunena pano makolo athu amenyedwa ndikutchecheredwa chimanga chawo m’minda yawo kumati achoke adzipita ku malawi koma dziko la malawi palibe chomwe likulabadira pa nkhaniyi.

“Ndikunena pano mawanja ochuluka ndi omwe athamangitsidwa, minda yawo ndikutchetchedwa. Tangoganiza, ino ndi nthawi ya mvula, nthawi yolima ngati ino anthu kuthamangitsidwa mwachipongwe minda yokhala yawo sir nthawi yotha kale ngati imeneyi anthu akalima kuti?” wadabwa munthuyo.

Munthuyu anapitilira ndikunena kuti anthu ambiri a midzi yomwe ikupanga zimenezizi ndi omwe anabwera kudzapempha malo okhala ku delari pa nthawi yomwe ku Mozambique kunali nkhondo ya pachiweniweni.

Poyankhula ndi tsamba lino, mfumu yaikulu Makanjira yomwe inabadwa Akib Ali yati ndiyodandaula kuti anthu amdera lake akuzuzidwa ndi apolisi a mdziko la Mozambique pa nkhani ya malireyi ndipo yapempha akuluakulu a boma omwe akuti m’mbuyomu anawalonjeza kuti adzapita kudelari kukalongosora za malirewa, kuti achite machawi ponena kuti zinthu sizili bwino.

Iwo ati anakakonda anthu amdera lawoli aziloredwa kulima kufikira pomwe akuluakulu a mayiko awiriwa adzakumane ndikukambirana za nkhaniyi ndiposo apempha kuti dziko la Malawi litumize asilikali omwe adzikateteza nzika za dziko lino zomwe akuti zikukhalira kuzuzidwa ndi asilikali komaso anthu a mdziko la Mozambique.

“Anthuwa akhala akulima malowa kwa zaka zambiri, nde ife timadandaula kuti anthuwa alime chaka chino kenaka akakolora chimangacho asiye pomwe tikudikira kuti akuluakulu athu akambirane za malirewa. Kagawidwe ka malo sikanali bwino koma anatiuza kuti abwera kudzakonza nde ndi zomwe ife tikudikira. Choncho tikupempha pomwe tikudikilira kudzakonzaso malirewa, apolisi athu ena akakhale ku malireko chifukwa kumeneko ndikumene kukuvuta kwambiri.

“Kunali mabikoni oyamba koma ena anawachotsa ndikuika awawa amene analowa nkati kwambiri mwa dziko lino komabe ma bikoni ena anakalipo amaoneka. Ife tikupempha kuti chonde akuluakulu athu tithandizeni, afulumile abwere kuti nkhaniyi ithetsedwe,” yapempha mfumu yaikulu Makanjira.

Ina mwa midzi yomwe yokhudzidwa ndi nkhaniyi ndi monga: Makunula, Mkopiti, Madi, Lukono, Ngwati, Bonazani ndi midzi ina yambiri.

Advertisement