DPP ikutinji lero? Atatu awonekera ku komiti yosungitsa mwambo

Advertisement
Cecilia Chazama of the Democratic Progressive Party

Lero komiti yosungitsa mwambo ku chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) yakumana ndi a Kondwani Nankhumwa, Mark Botoman komaso a Cecilia Chazama koma osewa sakuulura momwe zathera, pamene a Grezelder Jeffrey sanafike kumaloku.

Anayiwa anaitanidwa ku komiti yosungutsa mwamboyi kuti mwa zina akafotokoze bwino zifukwa zimene anaitanitsira komaso kuchititsa mkumano wa akuluakulu a chipani, National Governing Council (NGC) ku Lilongwe kumapeto a mwezi wa November, 2023, popanda kudziwitsa mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika.

Oyambilira kuonekera ku komiti yosungutsa mwamboyi lero Lachinayi pa 4 January, 2023 ku hotela ya Golden Peacock munzinda wa Lilongwe, anali a Mark Botoman omwe anatenga nthawi yopitilira ola limodzi ali muchipinda chomatacho ndipo atatuluka anakanitsitsa kuti sangafotokozere atolankhani nfundo zomwe zinamanga nthenje pa nkumanowo.

Atatuluka a Botoman, analowamo ndi mayi Chazama ndipo nawoso anakhala munchipinda chomatacho nthawi yopitilira ola limodzi ndipo nawoso atatuluka momwe mumachitikira zokambilanazo, nawo anamenyetsa nkhwangwa pamwala kuti sabenthula zomwe zakambidwa pa nkumano wawo ndi akuluakulu osungitsa mwambowo.

Omaliza anali a Nankhumwa koma iwowa mosiyana ndi anzawo onse anatenga nthawi yochuluka kwambiri, kupitilira maola awiri koma nawoso pomwe amatuluka munchipinda chomatacho anakana kufotokozera atolankhani zomwe agwirizana pa zokambiranazo ndipo anali chipani ndi chomwe chingafotokoze.

Pomwe aliyese amayembekzera kuti omaliza kuonekera ku komiti yosungitsa mwamboyi akhala mayi Jeffrey, iwo sanafike kumalowa ndipo sizikudziwika ngati iwo apeleka zifukwa zili zonse zomwe sanapezekele pa zokambiranazi.

Pakadali pano, maso a anthu ali akuluakulu a chipani cha DPP kuti afotokoze zina mwa zinthu zomwe agwirizana ndi makosanawa pa zokambirana zomwe komiti yosungitsa mwamboyi inachititsa ndi anthu atatuwa.

Advertisement