Mu 2024 tikankhe, atero a Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera president of Malawi

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati mu chaka cha 2024 ndikofunika kukankha kuti zinthu ziyende bwino ndipo wachenjeza kuti kukankha kwina ndikuchotsa anthu omwe akungowononga ndalama mu maofesi aboma.

A Chakwera amayankhula izi pa 31 Disembala, 2023 mu uthenga wake womaliza wa mu chaka cha 2023 pomweso anafunila a Malwi chaka chopambana cha 2024.

Malingana ndi a Chakwera, chaka chatsopanochi ndichofunika kukankha kuti mapolojekiti amene anayamba kale amalizike ndipo ena ayambe komanso kuti pagwilidwe ntchito ya phindu.

A Chakwera anati chaka chimenechi kuli ng’amba ndipo ndikofunika kuonetsetsa kuti anthu akudzala mbewu zokhazo zomwe zingachite bwino mu nyengo ya ng’amba.

Iwo anaonjezeranso kuti popeza boma lawo mu 2023 linaika njira zosamalira chuma cha dziko lino, ndikofunika kuonetsetsa kuti zonse zomwe zimachitika mwachisawawa zikankhidwe ndipo zichoke mu 2024.

“Kaya kutanthauza kuchotsa anthu chifukwa akungotaya nthawi m’maofesi kapena akungotaya ndalama m’njira yachisawawa yosafuna kutumikira a Malawi, tikankhe anthu oterewa ndipo kukankha kwakenso sikuti tizizipesa kwa wina aliyenseyo ayi,” anatero a Chakwera.

Mu mawu awo, a Chakwera anati 2023 inali ndi zambiri zokhoma monga nthenda ya kolera, kunali chilala komanso kunali vuto la Cyclone Freddy zomwe Malawi inayesetsa kugojetsa chifukwa cha kugwilizana. Iwo anaonjezera kuti boma lawo mu 2023 linathananso ndi kuzimazima kwa magetsi.

Pa nkhani ya njala yomwe yavuta mdziko muno, a Chakwera anati ndalama za mtukula pakhomo zikuperekedwa kwa anthu oposa 7 million ndipo boma laika ndalama zokwana K30 billion zogulira chimanga komanso lapereka zipangizo zotchipa mtengo monga fetereza ndi mbewu.

A Chakwera ananenso kuti kugwa kwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha kwapangitsa mitengo ya zinthu kuti zikwere koma kwathandizanso kuti dziko la Malawi liyambe kupeza ndalama zakunja kuchokera ku IMF zomwe zalimbikitsa ena kuti ayambe kupereka ndalama zowonjezera ku bajeti ya dziko.

“Ndipo mu bajeti yathu, taonetsetsa kuti a Malawi apeze popumira popeza taonjezera malipiro komanso tanena kuti a malonda asaonjezere mitengo ya zinthu mokuswa malamulo,” anatero a Chakwera.

Advertisement