Wapha mzake pa khilisimasi pomumenya ndi khasu m’mutu

Advertisement

Apolisi ku Kasungu anjata bambo wina wazaka 29 wina yemwe akumuganizira kuti anapha mzake wazaka 28 dzana pa khilisimasi pomumenya ndi khasu m’mutu.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Joseph Kachikho ati bambo yemwe akumuganizira kuti adapha mzakeyu ndi a Yamikani Mlotha ndipo ophedwayu ndi a Paul Banda.

Nkhani yonse ikuti awiliwa anapita ku malo ena ochitira malonda komwe adali kupapira bibida pa msika wina otchedwa Mphungu ndipo pobwerela kumalo omwera mowawa adasemphana chichewa zomwe zidadzetsa kusamvana mpakana kusinthana zibakera.

Ndipo awiliwa ali mkati mosinthana zibakera, Mlotha adatenga khasu ndikumumenya nalo mzakeyo mpaka kufero pomwepo kamba kakuti adali atataya magazi ochuluka kwambili.

Izi zinachitikira m’mudzi wa Kanselema kwa mfumu yayikulu Lukwa m’bomali.

Posachedwapa mkuluyu akawonekera ku bwalo lamilandu kamba koganizilidwa kuti adapha munthu.

A Mlotha amachokera m’mudzi wa Msungandewu kwa Lukwa komwe.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement