Maanja 28 ali kakasi kamba kamvula ya mphamvu yomwe yawononga katundu osiyanasiyana

Advertisement
A house in Kasungu in central Malawi

Maanja okwana 28 akusowa mtengo ogwira kamba ka mvula ya mphamvu yomwe yawononga nyumba komanso katundu osiyanasiyana kwa gulupu Mawawa, mfumu yayikulu Chulu m’boma la Kasungu.

Mwakatundu wina wawonongeka kamba ka mvula ya mphamvuyi ndi monga feteleza, mbewu, chimanga, ufa komanso nyumba  zomwe zagwa ndikusasuka madenga.

Malingana ndi anthu ena omwe akhudzika ndi mvula yamphamvuyi, iwo ali kakasi ndipo sakudziwa kuti tsogolo lawo komanso moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ukhala otani pamene mvulayi yawononga zinthu zomwe zikanatha kuwathandiza pa miyoyo yawo.

Kamba kavuto lomwe anthuwa lawagwera, iwo apempha anthu onse omwe ali akufuna kwabwino kuti awathandize ndi thandizo monga chakudya, mapepala apulasitiki, ndi  zovala kuti zithe kuchepetsako mavuto omwe akukumana nawo kamba kavutoli.

Pakadali pano akuluakulu komanso adindo mbomali sanayankhulepo pa zankhaniyi.

Mvula ya mphamvu ikupitilira kuwononga katundu osiyanasiyana ndipo pakadali pano ena mwa maboma omwe akhudzika ndi monga Salima, Kasungu ndi ena.

Advertisement