Malaulo: Mfumu yapereka pathupi kwa mwana wazaka 16


Zina ukamva ngati kumaloto ndithu. Apolisi m’boma la Kasungu amanga mfumu Mwimira yazaka 52 kamba  kogwilira mdzukulu wake wazaka 16 ndikumpatsanso pathupi.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Joseph Kachikho, makolo amwanayu anadabwa kumuona mwanayu akuwoneka kuti ali ndi pathupi  koma mwanayu samanena yemwe anampatsa pathupipo.

Atamupanikiza ndi mafunso, mwanayu adawulula kuti pathupipo adampatsa ndi mfumuyi yomwe dzina lake lenileni ndi a Hendreson Mwale.

Ndipo mfumuyi yakhala ikuchita zamalawulozi ndi msungwanayu kuyambira mchaka cha 2018 apa mkuti mwanayu ali ndi zaka 11 zakubadwa.

Msungwanayu atamutengera kuchipatala kuti akamupime, zotsatira zinaonetsa kuti ali ndi pathupi.

Posachedwapa mfumuyi ikuyembekezereka kukaonekera kubwalo lamilandu ndi kukayankha mlanduwu.