Khoti ku Zomba lalephera kuyamba kumva mulandu wa Bon Kalindo

Advertisement

Bwalo la milandu ku Zomba lalephera kuyamba kumva mulandu wa mkulu wa bungwe la Malawi First a Bon Kalindo ndipo bwaloli lati mulanduwu uzayamba kumvedwa mwezi wa January chaka cha mawa.

A Kalindo  amayenera kukawonekera ku bwalo la mulandu lero Lachitatu ku Zomba koma bwalo lalephera kuyamba kumva mulandu wao chifukwa Principal Resident Magistrate Martin Chipofya yemwe akumva mulanduwu sakupeza bwino mthupi.

Loya yemwe akuyimilira a Bon Kalindo pamulanduwu Timothy Chirwa wati alandira uthenga kuchokera kwa kalaliki  waku bwalo lamilandu kuti mulanduwu wayamba wayima kaye popeza a Principal Residents Magistrate sakupedza bwino choncho awapatsabe masiku omwe mulanduwu udzayambe.

A Kalindo adawamanga chifukwa chowaganizira kuti adayambitsa zipolowe pa ziwonetsero zomwe adachititsa ku Zomba pa 3 November.

Tilipa nkhani ngati yomweyi, bwalo la milandu  ku Mangochi likuyembekezeka kudzayamba kumvanso mulandu wa a Bon Kalindo pa 11 January chaka cha mawa pamulandu omwe akuwaganizira kuti adayambitsa zipolowe ku Mangochi panthawi yomwe amachita ziwonetsero

Advertisement