Mneneri Phiri wapezeka olakwa pa mlandu ochita za akuluakulu ndi mwana wake

Advertisement
Prophet Christopher Phiri of the Supernatural Embassy Ministry has appeared before a court in Mangochi today following his arrest on allegations that he sexually abused his daughter aged 16.

Bwalo lamilandu ku Mangochi lapeza olakwa m’neneri Christopher Phiri wa mpingo wa Supernatural Embassy pa mlandu oseweretsa malo obisika a mwana wawo wa mkazi zomwe akuti zinali ndi kuthekera koti anakagonana naye.

Apolisi kumapeto kwa mwezi watha, anamanga mneneri Phiri omwe ndi azaka powaganizira kuti amagonana ndi mwana wawo wa mkazi wa zaka 16 koma nkhaniyi itapita ku bwalo la milandu, panalibe umboni oti mkuluyu anachitadi kuseweruzikako.

Izi zinapangitsa kuti mbali ya boma ipemphe khothi kuti iwo akaunikenso milandu yomwe anawapatsa a Phiri ndipo bwaloli litakumanaso lachiwiri pa 19 December, 2023, a Phiri anawapatsa milandu iwiri; wina ochita zinthu zosayenera ndi mwana wachichepere zomwe mapeto ake akanatha kugonana naye komanso kuseweretsa malo obisika a mwana wachichepere.

Mbali ya boma inapeleka milandu iwiriyi kwa a Phiri potengera umboni omwe anapeza omwe ndi zithunzi komanso kanema yemwe apolisi anapeza mu telefoni ya mmanja ya mneneriyo.

Atapatsidwa mwayi kuti akane kapena kuvomera milandu iwiriyi, munthu wa mulunguyu sanachedwechedwe koma kuvomera kuti inde anachitadi zomwe bwalolo limawaganizirazo ndipo pomwepo apezeka olakwa pa milandu iwiriyo.

Bwaloli lati lidzapereka chilango kwa a Christopher Phiri omwe amachokela mmudzi mwa Manjawira kwa mfumu yaikulu Phambala m’boma la Ntcheu, pa 29 December, 2023.

Advertisement