A Ken Msonda apepesa kwa a Mutharika

Advertisement
Ken Msonda, Jappie Mhango and Joseph Mwanamvekha

A Ken Msonda omwe ndi membala wa komitiyi yaikulu ya chipani cha DPP apepesa kwa mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika pa zomwe iwo akhala akuchita ndipo pano ati akufuna a Mutharika atengenso mpando wa mtsogoleri wa chipani cha DPP.

Izi zadza pomwe lero a Mutharika anayankhula mozaza ndikuwadzudzula a Msonda kuti akhoza kubwerela ku chipani chawo chakale. A Mutharika anati a Msonda akhala akumatenga ziletso ku khoti zomwe zikusokoneza DPP.

Poyankhulapo, a Msonda anapepesa ndipo anati chipanichi chikufunika munthu ngati a Mutharika kuti atsogolele kuti chibwelereso m’boma m’chaka cha 2025.

Iwo anati mlandu omwe unalipo omwe iwo ndi anthu ena anakamang’ara kuletsa a Mutharika kudzaimaso pa komveshoni yomwe ikuyembekezeka kuchitika chaka chino anawuthetsa kutelo kuti a Mutharika ndiwoloredwa kutelo.

“Zimene tinapanga ifeyo atatu, tinamuuza loya kuti tathetsa mlandu. Lero kulibe mlandu, muyima chifukwa ife tinathetsa mlandu, muyimaso. Ine mpakana lero ndi ali ndisanasankhe kandideti chifukwa timadikira inuyo,” watelo Msonda.

Pakadali pano a Msonda ati maso awo ali patsogolo kulimbikitsa kumanga chipani cha DPP.

Lero chipani cha DPP motsogozedwa ndi mtsogoleri wa  chipanichi a Peter Mutharika chinachititsa msonkhano wa chipani ku Mangochi.

Advertisement