FAM yakanira Wanderers kulepheretsa masewero ndi Silver Strikers mawa

Advertisement
Mighty Wanderers

Pomwe timu ya Mighty Mukuru Wanderers inatulutsa kalata lachiwiri yopempha FAM kuti ilepheretse masewero ake ndi timu ya Silver Strikers mawa pomwe yati ikufuna chilango chomwe yapatsidwa chiunikilidwenso, bungwe la FAM lakana pempholi ndipo lanenetsa kuti mawa ulipolipo wa nkhodzo za pusi pa bwalo la Kamuzu.

M’mawa walero, lachiwiri timu ya Wanderers inatulutsa kalata yonena kuti siyisewera masewero a ndime yachiwiri mu Airtel Top8 mpakana chilungamo chioneke pankhani ya chilango chomwe bungwe la FAM linapeleka ku timuyi potsatira chipwilikwiti cha masewero ake oyamba ndi timu ya Silver Strikers miyezi yapitayo.

Timu ya Wanderers kudzera mwa m’modzi mwa akuluakulu ake a Roosevelt Mpinganjira anati iwo akufuna kuti masewerowa ayime kaye kamba koti akufuna kuti nkhaniyi itsatidwe bwino bwino ndipo chilungamo chiwoneke pa chilango chomwe timuyi ikuti sichoyenera.

Mu chikalata chake, timu ya Wanderers yati ndiyodabwa kuti bungwe la FAM silikuona kuti vuto lonseli linabwera kamba kawoimbira Godfrey Nkhakananga yemwe anavomera kuti Silver yachinya chigoli cha chiwiri pomwe iye yemwe anali ataimba kaleso kuti kunali kukankhana kankhana.

Koma malingana ndi kalata yomwe bungwe la FAM latulutsa yomwe yasayinidwa ndi a Alfred Gunda, masewero achiwiri a timu ya Wanderers ndi Silver, akhalapobe lachitatu lino pa bwalo la masewelo la Kamuzu munzinda wa Blantyre monga momwe anakozedwera poyamba.

Advertisement