Ntcheu Sekondale ayitseka kaye

Advertisement

Potsatira ziwawa zomwe ophunzira apa sukulu yaboma yogonera konko ya Ntcheu sekondale anachita lolemba, unduna owona za maphunziro m’dziko muno, watumiza ophunzira onse pasukuluyi ku tchuthi chokakamiza.

Lolemba masana, pa 27 November, 2023 ophunzira ena pasukuluyi anayamba kugenda magalasi a malo ochitira zinthu zosiyanasiyana (hall) komaso ma ofesi a mphunzitsi wa mkulu pokwiya ndi zomwe a kuti akuluakulu a sukuluyi anachitira ophunzira anzawo ena.

Malipoti akusonyeza kuti akuluakulu a sukuluyi anaimitsa kaye ophunzira anayi a fomu folo (form four) pa sukuluyi chifukwa chopezeka olakwa pa mlandu ozunza ana a fomu wani (form one) mu dzina la tizi (tease).

Pokhudzidwa komaso kukwiya ndikuyimitsidwa kwa ophunzira anayiwa, ophunzira ena a fomu folo anayamba kuvumbulutsa miyala kulunjika ofesi ya mphunzitsi wa nkulu komaso holo ya sukuluyi zomwe zinapangitsa kuti chili chose chisokonekere pa sukuluyi.

Potsatira izi, apolisi anaitanidwa kuti adzasungitse bata pa sukuluyi ndipo nawo anangofikira kuthira utsi okhetsa misozi pa sukuluyi zomwe zinapangitsa kuti bata lisokonekele pa sukuluyi kamba koti ophunzira olakwa ndi osalakwa omwe kunali phazi thandize.

Ophunzirawa amathawira m’midzi yoyandikira monga Gumbu, Kandota, Kachimanga ndi ina kamba koti sakanatha kupilira ndi utsi okhetsa misoziwu.

Patapita nthawi pang’ono unduna wa maphunziro kudzera mwa mphunzitsi wankulu pa sukuluyi a Jilesi Puma, analengeza kuti sukuluyi yayamba yatsekedwa kaye kufikira mtsogolomu pomwe chiganizo china chipangidwe ndi akuluakulu a maphunziro m’dziko muno akamaliza kafukufuku wawo pa zomwe zachitikazi.

Malingana ndi a Puma, undunawu watseka kaye sukuluyi ponena kuti potsatira zomwe zachitikazi pasukulupa palibe chitete zomwe anati zitha kuika miyoyo ya ophunzira ena pachiopsezo ndipo ophunzirawa anauzidwa kuti pofika lachiwiri m’mawa nthawi ya 6 koloko, aliyese akhale atachoka pasukuluyi.

Ophunzira omwe amachokera madera oyandikana ndi sukuluyi anyamula katundu wawo kupita mmakwawo lolemba lomwelo pomwe ena ochokera kutali agona pasukulu pomwepa ndipo akuyembekezeka kufika mmakwawo lero lachiwiri.

Posachedwapa, unduna wa za maphunziro unatsekanso sukulu yasekondale ya Nachitheme m’boma lomweli la Ntcheu pomwe ophunzira enaso kumeneko anaononga katundu pasukulupo.

Advertisement