Anthu atatu akuganiziridwa kuti adaba malata ku Police College

Advertisement

Bwalo la Senior Resident Magistrate ku Zomba latulutsa pa belo anthu atatu omwe akuganidziridwa kuti adaba malata ku Police College pa 26 November panthawi ya zipolowe zomwe zidabuka pakati pa apolisi ndi anthu okhala mamdera a Chikanda, Mpondabwino, Kazembe ndi Chilupsa pomwe apolisi adaphulitsa utsi okhetsa misozi.

Bwaloli lakananso kupereka belo kwa anyamata ena awiri omwenso akhudzidwa ndi nkhaniyi ati chifukwa chowakayikira kuti akhodza kuthawa akawapatsa belo ati chifukwa adasintha zoyankhula zawo panthawi yomwe amawafunsa mafunso.

Oyimira boma pamilandu Inspector Rodrick Kamuona adawudza bwalo kuti lisapereke bail kwa anthu asanuwo popedza angathe kukasokonedza umboni popedza pakali pano apolisi akufufudzabe kuti apedze malata ena omwe adabedwa patsikulo.

Inspector Kamuona adati pakali pano malata omwe apedzeka omwe adabedwa pazipolowezo ndi andalama zokwana 480,000 kwacha.

Koma loya yemwe akuyimilira m’modzi mwa anyamatawo Humphrey Panchi adapempha bwaloli kuti lipereke belo kwa Tinkhani Masamba chifukwa ali pa sukulu ndili ndipo kumusungabe mmanja mwa apolisi kukhodza kuwononga mtsogolo lake lamaphunziro.

Koma popereka chigamulo chake chokhudza belo, yemwe akumva mlanduwu Senior Resident Magistrate Yohane Munthali adati ndi ufulu wamunthu kupempha belo komanso similandu yonse yomwe munthu akuganidziridwa kuti wapalamula angapatsidwe belo.

Pamenepa Senior Resident Magistrate Munthali adapereka belo kwa anthu atatu ndipo ena awiri awakaniza kuwapatsa belo ati chifukwa chowakayikira kuti akhodza kuthawa akawapatsa bail ndipo adalamula kuti anyamata omwe apatsidwa bail apereke 50,000 kwacha aliyense komanso adzikawonekera ku polisi pakatha masiku 14 aliwonse ndipo mulanduwu ukuyembekedzeka kudzayamba pa 7 December

Anyamata omwe apatsidwa bail ndi Hendrick M’bawa, Tinkhani Masamba ndi Misozi Matebule ndipo anyamata awiri omwe akanidzidwa bail ndi Joseph Mangungu komanso Masautso Maxwell.

Advertisement