Anjatidwa kamba kotukwana apolisi patsamba la mchezo la Fesibuku


Woman who allegedly insulted Malawi Police officers

Mayi wina wa zaka 24 zakubadwa m’boma la Nkhotakota watsekeledwa mchitokosi pa polisi ya Nkhunga kamba konyoza ndikutukwana apolisi kudzera pa tsamba lake la mchezo la Fesibuku.

Mayiyu yemwe dzina lake ndi Anastasia Kamanga, adatukwakwana apolisi kuphatikizapo makolo awo omwe adabereka a polisiwa pa tsamba la mchezo lotchedwa Zokonda Amai Macheza pamene iye amkadzudzula apolisi kuti ndi achinyengo.

Mayiyu akuganizilidwa kuti adatukwana a polisiwa mwezi uno pa 25, ndipo iye atazindikira kuti apolisi akumusaka wakhala ali akubisala kufikira lero pamene apolisiwa akwanitsa kumumanga

A Anastasia akuyembekezereka kukayankha mlandu otukwana a polisi kudzera pa tsamba la mchezo.

Mayiyu amachokera m’mudzi mwa Denja mfumu yayikulu Kanyenda m’bomali.

Wolemba: Ben Bongololo