A Malawi kudzaipatsa moto! Akusonkha ndalama yoti Mai Mbambande akamubwezere Triephornia Mpinganjira

Advertisement
Triephornia Bender is a Malawian businesperson married to tycoon Thom Mpinganjira

Ayambe kumbuyoko/Ayambe kumbuyoko kudzapeleka aaa/tiyeni tonse tikapeleke: Iyi ndi nyimbo yomwe akuimba anthu omwe alowa gulupu la pa ‘WhatsApp’ lomwe a kuti likusonkherana ndalama yoti Mai Mbambande akabweze kwa Triephornia Mpinganjira. Zoonadi, mbuto ya kalulu inakura nditadzaonani.

Nkhaniyi yayambika kumathero asabata komweku pomwe nkazi wa khumutcha Thomson Mpinganjira, a Triephornia Mpinganjira anadzudzula bungwe la Mai Mbambande lomwe limathandiza anthu okalamba kuti silinawathokoze pathandizo lomwe iwo apeleka ku bungweli kumayambiliro a mwezi uno.

Malingana ndi zomwe tsamba lino lapeza, mpungwepungwe wayamba pomwe bungwe la Mai Mbambande limasaka thandizo la ndalama yokwana K800,000 yoti akagulire malata oti akhome pa denga la imodzi mwa nyumba zomwe bungweli likumanga zomwe mudzikhalamo anthu okalamba ochokera madera osiyanasiyana.

Mayi Mpinganjira atawona uthengawu kudzera m’masamba anchezo, anakhudzika mtima ndipo pa 1 November chaka chino anapisa mthumba ndikuvumbulutsa 2.5 miliyoni kwacha yomwe anapeleka kuti ithandize ntchito yofunikirayi.

Koma chatsitsa dzaye nchakuti, mpaka pano a Triephornia akuti sanalandire chithokozo kuchokera kwa Mai Mbambande komaso sanaone uthenga uli onse othokoza oyikidwa m’masambaa nchezo a bungweli ndipo potsatira izi mayi okwatiwa ndikumbuyo komweyu anapita patsamba lake la fesibuku ndikulemba kuti uku sikukhala.

“Aliyense, Uthenga wachidule wothokoza pamasamba anu ndi zina mutalandira thandizo kuchokera kwa anthu omwe sanadzitchule, angayamikiridwe kwambiri.

“Mukapempha anthu kuti akuthandizeni ndikuyika ma nambala anu aku banki pamenepo, dziwani kuti anthu amatumiza ndalama ndipo ena safuna kudziulura.Mutha kugawana nawo chiyamikiro chanu cha thandizo lawo ndikudziwitsa ena kuti vuto lanu lathetsedwa. Komabe, ngati mutapempha mosalekeza thandizo lomwelo pamene ena akupatsani kale chithandizo chomwecho, anthu angayambe kudabwa chifukwa chomwe mukufunira thandizolo pomwe ena akupatsani kale,” inatelo mbali ina ya uthenga wa Triephornia omwe unalembedwa mchizungu.

Potsatira zomwe analemba mayi Mpinganjira-zi, mwini wake wa bungwe la Mai Mbambande Deborah Mbale anayankhapo kudzera mu kanema yomwe wajambula momwe anatsimikizadi kuti analandira yokwana 2.5 miliyoni kwacha.

Mbale anafotokoza kuti analephera kuthokoza pa chuma chomwe analandirachi kamba koti pa uthenga wa mu foni omutsimikizira kuti walandira ndalama, panalibe nambala yomwe anakatha kufufuza za yemwe watumiza ndalamazo kuti amuthokoze mwapaderadera pa chifundo chaka.

Potsatira nkhaniyi, anthu ena ayambitsa gulupu la ‘WhatsApp’ pomwe a kuti ayamba kusonkherana ndalama yokwana 2.5 miliyoni kwacha yomwe a kuti akufuna akamupatse Mbale ndi bungwe lake la Mai Mbambande yoti ikabwezedwe kwa mayi Mpinganjira.

Ngakhale kuti omwe apanga gulupuyi sanabwere poyera nkufotoza tchutchutchu pa ganizo lawo lotolera ndalama yoti Mai Mbambande akabweze kwa Triephornia, anthu ena m’masamba a nchezo ati mkazi wa mpondamatikiyu samayeneraso kubwera poyera ndikuulula kuti ndalamayo anatumiza ndi iyeyo ndipo ati izi zikutanthauza kuti munthuyu amathandiza pofuna kuyamikilidqa.

“Koma chilipo apa nchoti bwanawa tingosonkha 2.5 million yawoyo tiabwenzele. Munthu unena bwanji kuti ndalandira pomwe watumizayo sukumudziwa, uziti ndalama yachokela kwa ndani? Komanso mesa amapeleka ngati osadziwika dzina ndi chifukwa sanayimbe foni asanatumize ? Amafunanso munthu azibwera kugulu kumazati chani?

“Komanso manambal ake munthuyo ali nawo, osamuyimbila bwanji kumufunsa asanabwele ku Fesibuku? Kuthandiza kuti atamike osati ntima.

“Bwana Triephornia Bender Daza, ife Anthu ovutika pa Malawi tati tibwenze 2.5 million mwathandiza nayoyi, tiyalukile zina. Pepani osakwiya Nafe, tili pansi panu. Koma ingovungani account number yanu tiziponya limodzi limodzi. Mukhululuke bwana wathu. Mwanayu Anthu amamukhulupilila, wakhala aKuthandiza kwambili kwa zaka zambili kuti afike pomwe alipa. Wavutika. Basi akayaluke chifukwa inu mwasonkha? Eh bwana,” anatelo munthu wina pa fesibuku.

Tikunena pano, anthu akutsutsanabe za yemwe walakwitsa pakati pa Triephornia komaso Deborah. Pomwe ena a kuti Deborah amayenera kuuza anthu omutsata kuti walandira ndalama kuchokera kwa munthu osadziwika, ena a kuti mayi Mpinganjira alakwitsa poyibweretsa nkhaniyi ku gulu ponena kuti anakatha kungoyimba foni ku bungweli ndi kukambirana ku mbali komko.

Anthu enaso akudzudzula anthu omwe ayambitsa gulupu ya ‘WhatsApp-yi’ ponena kuti amenewa ndi amene akufuna akukulitsa nkhaniyi komaso kukolezera udani wa khoswe ndi mphaka pakati pa anthu awiriwa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.