Ana akufuna chipepeso powachita mdulidwe makolo asakudziwa

Advertisement
Circumcision Malawi

Ana okwana 312 m’boma la Phalombe akamang’ala ku khothi kuti bungwe la Family Health Services (FHS) lomwe m’mbuyomu limatchedwa Population Services International (PSI) liwapepese ndi ndalama kamba kowachita mdulidwe makolo awo asakudziwa.

Izi ndimalingana ndi nyuzipepala ya Weekend Nation yomwe yati anawa omwe ndiochokera mdera la mfumu yaiku Mkando, m’boma la Phalombe, anachitidwa mdulidwewu mu zaka za 2021 ndi 2022 pomwe bungwe la FHS lakhala likuyenda m’makwalala kulimbikitsa amuna kuti akachitidwe mdulidwe wa makono mu pulojekiti yotchedwa Voluntary Male Medical Circumcision (VMMC).

Nyuzipepalayi yati odandaula oyamba omwe akamang’ala za nkhaniyi kubwalo la milandu la Midima ku Limbe mumzinda wa Blantyre ndi a Damson Esimey, omwe ndi kholo la Enock Kachala, omwe akuti iwo sanadziwitsidwe komaso sanapeleke chilolezo kuti mwana wawo apite ku mpeni.

Malingana ndi zikalata zomwe anawa asumira bungwe la FHS, anawa anakafika ndikudulidwa ku chipatala cha Migowi m’bomali pomwe akuti anakopeka ndikuyamba kutsata galimoto yomwe inali ndi chinkuza mawu pmwe pamaseweredwa nyimbo zopatsa chikoka kwinaku ikuzungulira m’bomalo kumema amuna onse kuti akalandire mdulidwe.

A Dalitso Chimbe omwe akuimira ana onse 312, anatsimikizira nyuzipepela ya Weekend Nation kuti anawa akufunadi ndalama za chipepeso kamba kovulazidwa, kuikidwa mu ululu ndi kupatsidwa chilema zomwe a kuti ndizosemphana ndi gawo 30 la malamulo oteteza ana m’dziko muno.

A Chimbe anapitilira kufotokoza kuti makolo a anawa anali odabwa ndipo sakudziwabe mpaka lero cholinga chenicheni cha mdulidwewu omweso akuti siunali mdulidwe wa chikhalidwe kapena wa chipembedzo, ndipo ati anawo akufunanso kuti bungweli lilipire ndalama zimene zingagwiritse ntchito nthawi yomwe mlanduwo ukhale ukumvedwa kubwaloli.

“Odandaulawo (ana aang’ono) adakopeka ndi galimoto ndi nyimbo zake ndipo adatsatira galimotoyo kapena adakwera m’galimoto osapelekezedwa ndi owayang’anira.

“Magulu onse a odandaulawo adali pamasiku osiyanasiyana kenako adawatengera ku chipatala chaching’ono cha Migowi m’bomalo komwe wozengedwa mlandu adakhazikitsa malo ochitira mdulidwe wa amuna monga mwa polojekiti yomwe yatchulidwa kale m’mwambamu,” anatelo mbali ina ya chikalatacho.

Koma yemwe akuyimira bungwe la FHS pa mlanduwu a Francis Kaduya, ati bungweli likufuna litsutse mlanduwu ndipo ati iwo apempha khothi la Midima kuti lisamve mlanduwu chifukwa choti ena amene akufuna chipepeso akutero kamba ka ukathyali wongofuna kupeza ndalama posayenera.

Ngakhale bungwela FHS likutelo, aka sikoyamba kuti litengeledwe kukhoti pa nkhani za mdulidwe kamba koti chaka chatha, bwalo lalikulu la milandu ku Blantyre linapeza kuti bungweli ndi lolakwa pakuchita mdulidwe mwachisawawa kwa ana awiri achichepere osalandira chilolezo kuchokera kwa makolo kapena owalera.

Advertisement