Alimi ayamba kubzala ku Mpemba

Advertisement
Mvula Malawi

Alimi okhala ku Mpemba mu mzinda wa Blantyre, ali mkati mobzala mbeu nzawo kutsatira Mvula ya mphamvu yomwe inagwa m’derali mu usiku wa pa 9 November, 2023.

Bambo silika ochokera m’mudzi mwa Mkoma m’dera la mfumu yaikulu Mtonda mu mzinda wa Blantyre ndi m’modzi mwa alimi amene ali mkati mobzala mbeu zawo ndipo iwo ati akhutira ndi mvula yomwe yagwa yomwe yapatsa chilimbikitso choti adzale mbeu zawo.

“Tili ndi chikhulupiriro kuti mbeu zathu zimera bwino ndithu chifukwa mvula yomwe yagwa ndi yambiri ndipo pansi pali nyontho okwanira,” anatero bambo Silika.

Ngakhale izi zili chomwechi, boma kudzera ku unduna owona za nyengo ukuchenjeza alimi kuti asapupulume kubzala mwachangu mbeu zawo kaamba ka ng’amba yomwe ikhudze madera ambiri akum’mwera mu mwenzi uno wa November.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.