Wapolisi wayimitsidwa ntchito kamba ka kilipi yotchula Kunkuyu

Advertisement
Minister of Information Moses Kunkuyu speaking at a press briefing in Lilongwe on president Lazarus Chakwera's foreign trips

Apolisi m’dziko muno ayimitsa pa ntchito wapolisi nzawo a Inspector Susan Kachinga omwe akukhudzidwa ndi kilipi yomwe a Moses Kunkuyu anatchulidwamo kuti akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa Allan Wittika.

Sabata yatha, apolisi anamanga Inspector Kachinga komanso a Mercy Chiligo ndi Chipiriro Kalima powaganizira kuti ndi amene akufalitsa nkhani zabodza zokhudza kafukufuku amene akuchitika kutsatila kuphedwa kwa anthu ena mu Lilongwe kuphatikizapo a Wittika.

Atatuwa anamangidwa kutsatira kilipi (audio clip) ina yomwe anthu akhala akugawana m’masamba anchezo yomwe imafotokoza kuti nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu akudziwapo kanthu za imfa ya malemu Wittika mwezi wa September chaka chino.

Mzimayi yemwe akuveka mu kilipiyi anatchula Kachinga kuti ndi amene wakhala akuchita kafukufuku za kuphedwa kwa anthu angapo munzinda wa Lilongwe posachedwapa ndipo anafotokozaso kuti wapolisiyu yemwe anali ku nthambi ya zofufuza milandu (CID), ndi amene anauza anthu ena kuti a Kunkuyu akudziwapo kanthu za imfa ya Wittika.

Pomwe bwalo lamilandu la Blantyre Chief Resident Magistrate latulutsa anthu atatuwa pa belo masiku apitawa, nthambi ya polisi yaimitsa kaye a Kachinga pa ntchito yawo.

Malingana ndi chikalata chimene a kulikulu a nthambi ya Police ku Lilongwe atulutsa chomwe wasainira ndi wachiwiri kwa mkulu olemba anthu ntchito a Maxton Kalimanjira, mayi Kachinga ayimitsidwa ntchito kuyambira pa 1 November.

Posachedwapa mneneri wa Police mdziko muno a Peter Kalaya, anauza nyumba zina zofalitsira mawu kuti atatuwa akuyankha mlandu ogwilitsa ntchito makina a intaneti molakwika komanso kuononga mbiri yamunthu malingana ndi Electronic Transactions komanso Cyber-Security Act and Penal code.

Advertisement