Amai atatu komanso abambo 15 anjatidwa powaganizira kuti amaba mafuta mu sitima

Advertisement

Ofalitsa nkhani za Polisi ya Balaka, a Inspector Gladson M’bumpha, ati apolisi anjata anthu 18 omwe ndi kuphatikizapo amai atatu komanso mphongo 15 powaganizira kuti amaba mafuta mu sitima ya panjanji.

Malingana ndi a M’bumpha, oganizilidwawa adamangidwa m’bandakucha wa loweluka pa 28 October, 2023 m’mudzi mwa Kanono, mfumu yaikulu Symon m’boma la Neno.

A M’bumpha adafotokoza kuti izi zikudza pomwe akhala akulandira madandaulo okhudza kubedwa kwa mafuta kuchokera ku kampani ya maulendo apanjanji ya Central East African Railways (CEAR).

Potsatira kumangidwa kwa anthuwa, a M’bumpha afotokoza kuti apolisi akwanitsa kupeza mafuta a Diesel komanso Petrol okwana ma lita 300 komanso Ethanol okwana ma lita 200 yemwe akuganizira kuti ndi wina mwa katundu obedwayu.

Oganizilidwa mulanduwa awonekera kale ku bwalo la milandu komwe awatsekukira milandu yopezeka ndi mafuta popanda chilolezo komanso kupezeka ndi katundu yemwe akuganizilidwa kuti ndi obedwa.

Padakalipano, anthuwa ali pa limandi pa ndende ya Ntcheu kudikira kuti akawonekelenso ku bwalo la milandu popitiliza kuyankha milandu yawo.

Advertisement