Duncan ndi mamuna wabwino – watelo Tamia Ja

Advertisement
Tamia Ja (R) is a Malawian social media personality and comedian

…wati osamayankhulitsa chibwezi chikatha

Akayanjana: patangodutsa sabata zochepa ochita zisudzo Tamia Ja atasambwadza bwenzi lake Duncan Nyoni kuti ndi owumira, pano awiriwa abwelerana ndipo mkaziyu wayamikira kuti mamunayu ndi wabwino kwambiri.

Kuyambira sabata yatha pakhala pakuveka mphekesera kuti awiriwa omwe ubwezi wawo unatha mwezi watha, wabweleranaso; pajatu akuluakulu anati madzi samayiwala khwawa.

Tamia Ja yemwe anabadwa Hannah Jabesi watsimikiza kuti wabwelerana nduna Nyoni lachinayi pa 19 October, 2023 pomwe amacheza ndi Felistus Nya-uyu Ngwira patsamba la fesibuku.

Iye wati iyeyo ndi amene anayambitsa kuti awiriwa abwelerane pomwe akuti masiku ambuyowa anamutchayira lamya Nyoni kumuuza kuti akufuna akumane naye, wamusowa zedi.

“Ya tabwelerana, ndinanena kuti tathana chifukwa ndinali nditakwiya komaso kusweka mtima komaso kuti ndiziona anthu akukamba za ine pa masamba anchezo, nde zinangondibalalitsa.

“Ndinayamba ndi ineyo kumuimbira foni, ndimangomupatsa moni nde kenaka ndinamuuza kuti tikumane ndakusowa. Ndimamukonda kwambiri munthu uja ndipo zimene ndinkapanga zija naye ankadziwa kuti ndinkapanga chifukwa ndinali nditakwiya,” anatelo Tamia.

Ochita zisundzoyu wati pano amadandaula kwambiri akakumbukira chipongwe chomwe anamuyankhulira Nyoni pomwe ubwenzi wawo unatha koma anatsindika kuti zambiri ankayankhula kamba kopsa mtima.

Apa Jabesi wapepesa kwa bwezi lakelo lomwe limadoda chikopa mu timu ya Silver Strikers ndipo wapempha kuti amukhululukire pa m’nyozo omwe anayankhulawo.

Atafusidwa kuti anenepo kanthu pa zomwe anayankhula kuti Nyoni ndi owumira kwambiri, Tamia anaka kuyankhapo koma anayamikira kuti bwezi lakelo ndi mamuna wabwino.

“Duncan ndimamuna wabwino koma funso loti ndi owumira kapena ayi sindiyankha. Ndinapanga zimenezo kuti ndidziteteze ndekha koma kuchokera pansi pa mtima munthu uja ndimamukonda nayeso amadziwa koma ndimadandaula chifukwa sindimayenera kupanga zimene zija.

“Duncan ndimamukonda ndipo ndine wa chisoni ndi zomwe ndinapanga, ndikupepesa kuchokera pansi pa mtima,” anateloso Tamia.

Iye watsutsa mphekesera zomwe zikumveka kuti wabwelerana ndi Nyoni kamba koti ali ndi pakati, ndipo wauza anthu kuti ayembekezere ukwati posachedwapa.

“Ine siwoyembekezera, potha pa miyezi 9 mwina mumva za ukwati osati za mimba kapena kuti kwabadwa mwana,” wakana Tamia.

Pakadali pano nyenyeziyi yalangiza amayi komaso anthu onse m’dziko muno kuti azichepetsa ukali ndinso kulubwalubwa pamene ayambana ndi okondedwa awo komaso wati sibwino kulowelera nkhani za anthu omwe ali mu chikondi.

“Malangizo anga ndi awa; mukakhala kuti mwayambana ndi amuna anuwo, osamatha mawu chifukwa za mawa sizidziwika komaso osamalowelera nkhani za anthu omwe ali mu chikondi, sizikukukhudzani. Azimayi osamayankhulitsa, kumadekha,” walangiza choncho Jabesi

Advertisement