Imwani Kombucha mosalekeza mulibe bibida, simudzaledzera – atelo opangawo

Advertisement
It has been alleged that Kombucha drink contains higher alcoholic content than what is stated on the bottle

Fisi anakana nsatsi: kampani yopanga zakudya ndi zakumwa ya Nutricom Foods and Beverages, yakana mwantu wagalu kuti chakumwa cha Kombucha chomwe imapanga muli mphamvu yoledzeretsa.

Nkhaniyi ikudza pomwe kampaniyi ikudzudzulidwa kuti chakumwa chawo cha Kombucha muli mphamvu yoledzeretsa mpaka kufika mlingo wa 8 pelesenti (percent).

Nkhaniyi yawululika pomwe nyuzipepala ya The Nation inachita kafukufuku yemwe anapeza kuti zakumwa za Kombucha zina mukupezeka mphamvu yoledzeresa kufika mpaka 8 peresenti.

Mu nyuzipepala ya Lamulungu, The Nation, inanena kuti idatengera Kombucha mungapo ndikupita naye kukamuyeza komaso kukamuwunika ku sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences (Mubas) mumzinda wa Blantyre.

Nyuzipepalayi inalemba kuti pambuyo poyeza ndikuwunika zakumwazi, Kombucha wina adawonetsa kuti muli mphamvu ya mowa yokwana 7.35 peresenti pomwe Kombucha wa jinja (ginger) anali ndi mpamvu ya mowa yokwana 5.09 peresenti.

Izi ndikulekana ndi mphamvu ya mowa yokwana 0,005 peresenti yomwe kampani ya Nutricom Foods and Beverages imasonyeza pa mabotolo a zakumwazi.

Potsatira vumbulutsoli a Malawi ochuluka adandaula ndi nkhaniyi pomwe ena akuyikira umboni kuti analipitsidwapo zindapusa ndi apolisi a pansewu atayezedwa ndikupezeka kuti mthupi mwawo muli mphamvu ya mowa pomwe anali atamwa chakumwa cha Kombucha.

Koma poyankha za nkhaniyi kudzera munchikalata chomwe chatulutsidwa lolemba, kampani ya Nutricom Foods and Beverages yati chakumwa chawo cha Kombucha chakhalapo zaka 7 ndipo bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) yakhala ikuyeza ndikupeza kuti mulibe mphamvu ya mowa.

Kampani ya Nutricom Foods and Beverages yati nkutheka kuti mphamvu ya mowa yomwe The Nation yapezayi, imapangidwa potengera ndi malo omwe omwe Kombuchayo amasungidwa akafika pa nsika kuchoka ku fakitale.

“Pankhani yamitundu yosiyanasiyana ya mowa, tiyenera kutsindika apa kuti pamene tikupanga, mphamvu ya mowa mu chakumwachi ndi 0.005 monga momwe zimasonyezedwera pa mabotolo.

“Ngakhale zili choncho, potengera kusiyana kwa masungidwe a chakumwachi chikafika pa nsika, zikhoza kuchititsa kuti ntchito yakupangidwa kwa mphamvu ya mowa kuzipitilirabe zomwe zingapangitse kuti mphamvu ya mowa ikhale yosiyana ndi yomwe tinapanga ku fakitale,” yatelo kampaniyi.

Apa kampani ya Nutricom Foods and Beverages yatsindika kuti ilibe mphamvu pa momwe zakumwa zawo zingamasungidwire zikafika pa nsika kuchoka ku fakitale yake.

Kampaniyi yati ipitilirabe kugwira ntchito mosatopa ndi mabungwe onse oyeza katundu as anafika pa nsika ndicholinga choti kampaniyi ipitilizebe kupanga chakumwa cha bwino cha Kombucha monga yakhala ikuchitira mu zaka 7 zapitazo.

Advertisement