Atoht Manje wamwalira atamaliza kuimba

Advertisement
Munthu' hitmaker Atoht Manje real name Elias Missi has died.

Thambo lakuda lakuta dziko la Malawi pomwe lataya m’modzi mwa akatswiri oyimba nyimbo za lokolo Elias Misi, yemwe amadziwika ndi dzina loti Atoht Manje.

Malingana ndi zomwe tsamba lino lapeza, Atoht Manje wamwalira m’bandakucha wa Lamulungu ku sukulu yaukachenjede ya Livingstonia munzinda wa Mzuzu komwe kunali phwando la mayimbidwe.

Mphekesera zikuveka kuti atamaliza kuimba ku maloku, katswiriyu yemwe anatchuka kwambiri ndi nyimbo ya ‘Munthu’, anadandaula kuti sakupeza bwino mthupi mwake.

Mwa zina zikuveka kuti Atoht Manje anamva kutentha kwambiri kwa ka nthawi kochepa ndipo anapita mgalimoto kuti akapume kaye komwe a kuti anthu anamupeza atakomoka.

Atathamangira naye ku chipatala, madotolo analengeza kuti oyimbayu anafika naye atamwalira kale.

Pakadali pano oyimba m’dziko muno komaso anthu ambiri ati ndiokhudzika ndi imfa ya Manje yemwe amathyakula nyimbo zolimbikitsa mtendere zomweso zinali za chamba chaka chake.

“Ndine okhudzika kwambiri. Imfa ndi yowawa. Ndamva kuwawa Malume,” wadandaula oyimba nyimbo zauzimu Thocco Katimba.

Naye mkhala kale pa maimbidwe Lucius Banda wati naye ndiodandaula ndi imfayi pomwe walemba pa tsamba lake la fesibuku kuti; “Ndi zomvetsa chisoni komanso zowawa.”

Pano a Malawi m’masamba anchezo akugawana zithunzi komaso makanema omwe Atoht Manje anajambulidwa pomwe amayimba ku phwando la maimbidwelo.

Advertisement