Mukamakamba za kupanda chitetezo mu dziko muno tikumangani – watero Zikhale

Advertisement
Malawi Homeland Minister, Ken Zikhale Ng'oma

Ati mukamva za anthu osowa, kenako kuzindikira kuti aphedwa, muzingokhala chete basi ndi kumati Chakwera 2025 boma. Ati kufalitsa nkhani za kusowa kwa chitetezo mu dziko muno mutha kupezeka nazo ku jele. Atero ndi a nduna a za chitetezo a Zikhale Ng’oma.

Polankhula pa msonkhano wa atolankhani umene anachititsa ku Lilongwe, a Ng’oma ati mu dziko muno muli chitetezo chokwana. Iwo ati nkhani za kuphedwa kwa anthu zisapereke mantha kwa a Malawi.

A Ng’oma anaitanitsa msonkhanowo anthu awiri ataphedwa mwa njira zodabwitsa mu mzinda wa Lilongwe sabata lathu. Lachitatu, thupi la a Alan Witika amene amagwira ntchito ku kampani ya Coca cola linapezeka mu galimoto. Amene anawachita chipongwe sakudziwika mpaka pano.

Pamene anthu adali ogwidwa ndi mantha, nalo thupi la Mayi Agnes Katengeza linapezeka mu mzinda wa Lilongwe atasowa pa chiweru. Matupi onse anasiyidwa mu galimoto ndipo okuba sanatenge galimotozo.

Imfa ziwirizi zagwedeza a Malawi pamene zikuoneka kuti mu dziko muno chitetezo kwenikweni mulibe. Pofuna kupereka chiyembekezo kwa a Malawi, a Zikhale adayitanitsa msonkhano wa atolankhani.

Koma mmalo mopereka chiyembekezo zinaonetsa kuti nawo ngati nduna nkhanizi zawasokoneza mutu. Ngakhale iwo adatsindika kuti apolisi akufufuza nkhanizi, anatembenukiranso atolankhani kuti asamalengeze nkhanizi. Ati zimayambitsa mpanipani.

Iwo adaonjezeranso kuti a Malawi amene akumalemba za nkhanizi pa masamba a mchezo zikuchitika ali pa chiopsezo choti atha kumangidwa.

Advertisement