Wode Maya wavula chinyawu; watulutsa kanema ali ku ndagala

Advertisement
Wode Maya visited an initiation camp in Malawi

Pomwe anthu omwe sizikuwakhudza amaletsedwa kupita ku malo alionse opangira chinamwali cha a yao, ndagala, anthu adzidzimuka kuti mlendo Wode Maya wa ku Ghana anakalowako mpaka kujambula kanema yomwe watulutsa pano.

Mlendo odza nkalumo kakuthwayu yemwe dzina lake lenileni ndi Berthold Winkler, posachedwapa anali m’dziko muno paulendo wake odzasilira zachilengedwe zomwe dziko lino linadalitsika nazo, ndipo atafika ku mpanje kuno anayendera malo osiyanasiyana.

Ena mwa malo omwe Wode Maya anafikako ndimonga ku nyanja ya Malawi komaso anali ndi mwayi okumana ndi anthu odziwika angapo kuphatikizapo khumutcha Napolion Dzombe, kungotchulapo ochepa chabe.

Kupatula apo, zadziwika tsopano kuti ulendo wa mkuluyu sunathere pompo koma kukafika malo ochitira chinamwali cha anyamata antundu wa chiyao komwe mwachidule amakutchula kuti ku ndagala.

Izi zatutumutsa a Malawi ena omwe kudzera m’masamba anchezo awonetsa kudabwa kwakukulu kaamba koti pa mwambo wake aliyese yemwe chinamwalichi sichikumukhudza samaloledwa kukafika ku malo opelekera mwambowo.

“Wodemaya mpaka anakalowa ku Jando nkubwerako bhobho. Tikanakhala Ife simukanaimva mpaka tikanavinidwa by force! Ndipo timavidiyo sitikanatenga. Mukanati tayalutsa dambwe!” watelo katswiri ochita ndakatulo Robert Chiwamba.

Munthu winaso yemwe anaikira ndemanga pa kanema yomwe Wode Maya waika pa tsamba lake la fesibuku, wati mkuluyu samayenera kuloledwa kujambura zochitika ku ndagalako.

“Anakulora bwanji kuti uloweko ndi foni yako? Amene anakuloleza kulowayo akuyenera kulandira chilango chifukwa chophwanya chikhalidwe chathu,” anatelo munthu wina muuthenga omwe anaulemba mchingerezi.

Kanema yomwe Wode Maya waika pa tsamba lake la fesibuku, ikuonetsa mkuluyu akufika ku ndagalako mwansangala kwinaku akumavina monyadira nyimbo za mchiyankhulo cha chiyao chomwe anamwaliwo amayimba.

Ngakhale ena sakukondwa, a Malawi ena ayamikira ponena kuti mu kanthawi kochepa komwe Wode Maya anali m’dziko muno, wavumbulutsa zinthu zambiri zomwe zina a Malawi ochuluka samazidziwa kose.

Advertisement