…wati ku Malawi anthu anamudziwa atasauka
…wati iye ndi Zeze ya ndiwo yawo ndi K500,000 pa sabata
Anthu m’masamba anchezo akunyinyilika ndi zomwe wayankhula nzimayi ochita bizinezi, Dorothy Shonga Nkhoma pophweketsa 100 miliyoni kwacha kuti sindalama yakanthu.
Shonga anayankhula izi loweruka madzulo nkatikati mwa pologalamu yapadera ndi wailesi ya Times komwe iye ndi bwenzi lake Zeze Kingston amafotokoza zambiri zokhudza moyo wawo komaso m’mene ubwenzi wawo unayambira.
Mkati mwa pologalamuyi, Shonga yemwe m’mbuyomu wakhala akudziwika ndi dzina la Cash Madam, anafusidwa kuti afotokoze zambiri zokhudza mlandu omwe pano unakali kukhothi okhudza kampani yake ya Vink Enterprise.
Apa ndi pomwe Shonga Nkhoma analavula zakukhosi ndi kunena kuti ku Malawi kuno sanagwire ndalama zeni kuyerekeza ndi nthawi yomwe anali m’dziko la Uganda.
Shonga anapitiliza ndikunyalapsa ndalama yokwana 100 miliyoni yomwe khothi likuganizira kuti kampani yawo ya Vink Enterprise inalandira mosatsata ndondomeko bwinobwino, ponena kuti iyi si ndalama yakanthu koma ndi nyenyeswa chabe.
“Mwina nditha kunena kuti ku Malawi kunoku munandidziwa nditasauka. Nthawi imene ndi ali Cash Madam weniweni, ndi ali m’dziko la Uganda. Ku Malawi kunoku simnapangeko ndalama zoti ndinganene kuti zinali ndalama. 100 miliyoni ndi ndalama? Imeneyo ndiyochepa kwambiri (peanut).
“Ine munandidziwa ku Malawi kunoku zinthu zanga zitayamba kutsika pang’ono koma kulipo komwe ndinapanga ma miliyoni amuma dola (dollar) osati ku Malawi kunoku chifukwa ine ndimagwira ntchito zambiri,” anatelo Shonga.
Nzimayiyu anapitilira ndi kufotokoza kuti pakadali pano akutakataka zochuluka zomwe zimamubweretsera ndalama pa moyo wake koma wati sangazitchule potengera zomwe wakumana pomwe m’mbuyomu anawulura za ntchito zomwe amagwira.
Iye anati anthu ambiri m’dziko muno ndi ansanje, ndipo ngati angadziwe zomwe wina akuchita, amapanga zothekera kumusokoneza ndikumukokera pansi ndipo wati pano anapanga chisankho chobisa zomwe zimamupezetsa ndalama.
Shonga Nkhoma anapitiliraso ndikutsutsa mwantu wa galu kuti Zeze akudya ndalama za donayi ponena kuti ngati bambo wa m’nyumba Zeze ndi amene amatulutsa ndalama komaso waulura kuti banja lawo limagwiritsa ntchito K500, 000 ngati ya ndiwo pa sabata imodzi.
“Ayi ineyo ndamene ndikudya za iyeyu (Zeze) ndipo amawauzaso anzake kuti nyumba yake ikhale yabwino, amafunika ndalama yokwana K500,000 pa sabata imodzi. Ine ndi odula, iyeyu ndi odula, miyoyo yathu ndiyodula,” anaonjezera Shonga Nkhoma.
Zeze ndi duwa lakeli awuza anthu omwe akuona ngati ubwezi wawo ndiwongoyeselera kuti awuponda ponena kuti iwo ayenda kale mtundu wautali ali limodzi choncho sakuona chinthu chomwe chingawalekanitse mophweka.
Awiriwa alengezaso kuti chinkhoswe chawo chikhala m’mwezi wa December chaka chino, pamene ukwati wawo ukuyembekezeka kuchitika chaka cha mawa.