Mkulu wina m’boma la Mulanje waona mbonawona atakanilira panyumba yomwe anapita kuti akabe katundu m’bandakucha walero.
Izi ndi malingana ndi kanema yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo yemwe akuonetsa mkuluyu atavala kabudula wankati yekha atakanilira pa nyumbayi.
Malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti m’bandakucha wa lero, tsizina mtoleyu yemwe dzina lake silinadziwike, anapita ku nyumba ina m’boma la Mulanje kuti akabe katundu.
Anthu ena omwe amafotokoza mu kanema yomwe anthu akugawana m’masamba anchezoyo, ati mkuluyu anakwanitsa kulowa m’nyumbayo momwe munali a mayi okha kamba koti abambo anali atapita ku ntchito.
Zikuveka kuti oganizilidwa kubayu ananyamula sikilini (screen) ndi katundu wina ndipo anayenda nyang’anyang’a mpaka anakwanitsa kutulukaso m’nyumbamo osagwidwa koma anaona zakuda atafika panja panyumbayo.
Anthu akuti kathyaliyu wapezeka atakakamira pa nyumba yobedwayo m’mawa wa loweluka zomwe zinapangitsa kuti anthu akhamukile kukaona malodzawo.
Zikuvekaso kuti atawona malodzawo, mayi wa m’nyumbamo anathyayira lamya amunawo omwe a kuti anafika kunyumbako koma a kuti chodabwitsa nchoti atafika pa nyumba yawoyi, abambowa sanakhalitse, anatengana ndi akazi awo nkuchoka panyumbapo.
Anthu akukhulupilira kuti mwini nyumbayi anayikoza nyumba yakeyi kuti anthu akuba asamakwanitse kutelo akabwera.