Apolisi ati mipingo ili ndi udindo wolangiza akhristu zakuyipa kodzimangilira

Advertisement
Malawi Police

Apolisi mu boma la Machinga apempha amipingo kuti pamene akulalikira mau a Mulungu kwa akhristu awo, asamalepherenso kukamba nkhani zokuyipa kwa imfa zobwera chifukwa chodzimangilira komanso kuyipa kwa kulanga okha munthu yemwe akuganiziridwa kuti wapalamula mulandu.

Mkulu wapolisi woona zachitetezo cham’madera akumudzi mi boma la Machinga, Sub Inspector Masautso Katemera, ndi yemwe wayankhula izi kumipingo ya Katolika, Muslim, Mpingo wa Akhristu ndi ina yomwe ikupzeka bomalo pomwe amalimbikitsa akhristu amipingoyi zakuyipa kwa imfa zobwera chifukwa chokudzimangilira komanso kupha anthu omwe akuwaganizira kuti apalamula milandu.

Katemera wapempha ansembe, abusa, ma sheik komanso akulu akulu amipingo yosiyanasiyana yomwe ikupedzeka mu boma la Machinga kuti pamene akulalikira nthawi yamapemphero asamalephere kulangiza nkhani zokuyipa kozimangilira komanso kupha anthu omwe akuwaganizira kuti apalamula milandu.

Pamenepa iye adapemphanso kuti akawona munthu akusonyeza kuti ali ndi nkhawa azimuyitana ndikucheza naye kuti amve zimene zikumuvuta mu mtima mwake komanso ndikumupatsa malangidzo oyenera.

“Ifa zobwera chifukwa chokuzimangilira komanso milandu yokupha anthu omwe akuganidziridwa kuti apalamula milandu ikuchulukira m’dziko muno choncho ndi chifukwa ife a police boma lino la Machinga tikufuna tidziwitse anthu zokuyipa kwa mchitidwewu,” adatero Sub Inspector Katemera.

Ndipo poyankhulapo, mkulu wampingo wa Church of Christ a Edward Sinja adathokoza apolisi a mu boma la Machinga chifukwa cha pulogalamu yawo yoyendera mipingo yosiyanasiyana ndikuwaunikira nkhani za imfa zobwera chifukwa chokudzimangilira komanso kuphana.

A Sinja adati awonetsetsa kuti panthawi yomwe akulalakira mau a Mulungu adzilangizanso a khristu awo zokuyipa kwa imfa zamtunduwu.

Apolisi a boma la Machinga akuyendera mipingo yosiyana siyana komanso mizikiti kumalangidza anthu zokuyipa kwa imfa zobwera chifukwa chokudzimangilira komanso kuphana potsatira kuchuluka kwa ifa za mtunduwu muno Mmalawi.

Advertisement