Kupsa pansi ndi pamwamba ngati chigumu; Multichoice yakweza mitengo ya DStv

Advertisement

…premium yafika pa K79,000 pa mwezi

Pomwe mavuto a za chuma afika posauzana, a Malawi omwe amakonda zowonerawonera, alimbe mthumba kaamba koti kampani ya Multichoice Malawi yalengezaso za kukwera mitengo ya ma pakeji a DStv.

Lachisanu pa 21 July, 2023 kampaniyi kudzera pa masamba ake anchezo, yalengeza kuti kuyambira pa 1 August chaka chino, mitengo yomwe makasitomala amapeleka pogula ma pakeji osiyanasiyana pa DStv, ikwera.

Muuthenga wake omwe omwe ukuoneka kuti wakwiyitsa ma kasitomala ake ambiri, kampaniyi siyinapeleke chifukwa chili chonse chomwe yabweretsera ganizo lake lokweza mitengo ya ma pakeji a DStv.

Multichoice Malawi yati pakeji yotchipitsitsa yomwe imatchedwa Kufewa, tsopano izigulidwa pa K7,500 kuchoka pa k6,800 pomwe yotsatilana nayo ya Access yachoka pa K10,200 kufika pa K12,500 ndipo pakeji ya Family yafika pa pa K19,500 kuchoka pa K16,400 pamwezi.

Mbali inayi, pakeji ya DStv yotchedwa Compact tsopano yachoka pa K27,500 kufika pa K33,000 pamene Compact Plus yachoka pa K43,000 kufika pa k51,000 ndipo mtengo wa pakeji ya Premium wachoka pa K67,000 kufika pa K79,000 pa mwezi.

Anthu ambiri omwe akuyikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la DStv, akunyinyilika ndi mitengo ya tsopanoyi.

“Dziko lake ili kukweza chonchi? Mmm mwaiphonya, Azam atilandire basi, DStv yanuyo azionera ndi Chakwera and his cabinet coz they are the ones who have got vindalama,” watelo munthu wina.

Munthu winaso wadabwa kuti bwanji kampaniyi siyinawaimbire ma foni ma kasitomala ake kuti imve maganizo osiyanasiyana pa ganizo la kampaniyi lobweretsa mitengo ya tsopanoyi yomwe ambiri akuti zili ngati kuthira tsabola pa chilonda.

“Apapa simwakweza osatiimbira thenifolo kuti mumve maganizo athu, nde mwezi wamawa muyelekeze kuimba kuti bwanji sindikulipira, mudzava mtedza maphwanga. Mwachenjera pogona tionana podzuka mawa lino,” wateloso munthu wina pa fesibuku.

Izi zikubwera pomwe m’mwezi omwe uno kampani ya Multichoice Malawi yalengezaso kuti kuyambira pa 1 August mitengo yolipilira ma pakeji a GOtv, ikhala ikukwera.

Mkati mwa sabata ino, mmodzi mwa akuluakulu a kampaniyi kuno ku Malawi a Zena Makunje, anauza atolankhani mu mzinda wa Blantyre kuti mitengo ya tsopanoyi ithandiza kuti kampaniyi ipitilire kutumikira bwino ma kasitomala ake.

Advertisement