Ku-Li-mbuli?: Siine mbava, aphwanya poti n’nawaletsa kupha wakuba – walira mwini loji ku Mulanje

Advertisement

…wati katundu wa ndalama zoposa K700 miliyoni wawonongedwa

A Edson Nachuma omwe ndi mwini wake wa malo ogona alendo omwe awotchedwa Lolemba a Edga’s ku Limbuli m’boma la Mulanje, akanitsitsa mwantu wa galu kuti iwo ndi mbava komaso chigawenga chowopsa mdelari.

Lolemba pa 26 June, 2023, kunali chipwilikiti m’dera la Limbuli, m’boma la Mulanje pomwe anthu okwiya awononga katundu wa ndalama zankhaninkhani ku Edgar’s loji (Lodge) poganizira kuti mwini wake ndimbava yotheratu.

Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga nchakuti usiku wa lamulungu pa 25 June, 2023, anthu ena omwe sakudziwika akhapa ndikupheratu munthu wina ochita malonda m’derali omwe azindikilidwa ngati a George Moninji.

Malipoti omwe tsamba lino lapeza akusonyeza kuti kutsatira imfa ya a Moninji, anthu kuderali anayamba kufalitsa nkhani kuti wachita chipongwechi ndi a Nachuma omwe ndi mwini wake wa Edga’s loji

Anthuwa a maloza chala a Nachuma kuti ku loji kwawo akumasunga mbava zikuluzikulu zochokera m’dziko la Mozambique ndipo ena ati mkuluyuso payekha ndi tsizinamtole yemwe akuti wakhala akutsogolera zauchifwamba ku derali.

Potsatira manong’onpng’owa, anthu anamemana ndikukhamukira ku malo ogona alendowa ndikuyamba kuphwanya zinthu, kuphatikiza apo, anthuwa awotchaso magalimoto ndikubaso wina mwa katundu ku lojiko.

Ngati kuti zonsezi zinali zosakwanira, anthuwa anapitaso kunyumba ya a Nachuma komwe akuti akaphwanyaso ndi kuba ma miliyoni a ndalama, zomwe mkuluyu amasunga

Koma poti utsi sumafuka popanda moto, kodi a Nachuma akutinji za nkhani? Poyankhula ndi kanema ya Mibawa mkulu oganizilidwayu, wapukusa mutu opanda nyanga kuti iye sakudziwapo kanthu pa za imfa ya a Moninji ndipo wanenetsa kuti iye sikathyali.

Iwo ati akuganiza kuti anthu awapanga chipongwechi kaamba koti sabata ziwiri zapitazo, iwo monga wapampando wa komiti ya chitetezo m’derali, analetsa anthu kupha wakuba wina yemwe anagwidwa akuba ku nyumba kwa nzawo wina.

“Ndavetsedwa kuti anthuwa anabwera kwa ine chifukwa choti tsiku limenelo ndinakana kuti munthuyo aphedwe. Ndi za bodza, palibe wakuba amene anawulurapo kuti ine ndimawatuma kapena kuti amandipatsa zinthu akapita kukaba.

“Ndikukanitsitsa, sinayambe ndagulapo chinthu chobedwa, ndipo sindinafikepo ku polisi kuti ndapezeka ndi zinthu zomwe zabedwa kwina kuli konse,” watelo Nachuma.

Iye anavomeleza kuti ali ndi mfuti yemwe wati ili ndi ma pepala ake bwino bwino koma watsutsa mphekesera zoti mfutiyo ndi yomwe zifwamba zomwe zinavutitsa mderali posachedwapa, zakhala zikugwiritsa ntchito.

“Mfuti imeneyi layisesi (licence) yake yatuluka sabata latha. Zikalata zake ndakapanga ku Lilongwe, ndakaitengera ku polisi ya Mulanje, a polisi ya Mulanje akudziwa bwino za mfuti imeneyi,” anawonjezera choncho Nachuma.

Mkuluyu anavomeraso kuti panthawi yomwe izi zimachitika, mkuti ku malo ogona alendowa kuli alendo ena ochokera m’dziko la Mozambique omwe wati galimoto zawo zawotchedwa ndi anthu okwiyawa.

“Kunabwera ma kasitomala omwe anagona aku Mozambique, magalimoto awo okwana inayi (4) onse awotchedwa. Kwaonongedwa katundu wa ndalama zoposera K700 miliyoni,” ateloso a Nachuma.

Iwo ati ndalama yokwana K27 miliyoni yomwe anthuwa akabaso ku nyumba kwawo, anali atalandira loweruka lapitali kuchokera ku kampani ya Chibuku komwe akuti anagulitsa chimanga ndipo amayembekeza kuti akayisiye ku bank Lolemba lomwe zinthuzi zachitika.

A Nachuma omwe akuti amachita malonda a mbewu zakumunda, adandaula kuti zachitikazi zawasokoneza kwambiri ndipo apempha Mulungu kuti awathandize.

Pofika madzulo Lolemba, apolisi amanga anthu anayi (4) ndi kupezanso ma sikilini (plasma screen) awiri ndi njinga yakapalasa imodzi.

Ena mwa anthu omwe amangidwawa ndi; James Rabana wa zaka 37 yemwe amachokera m’mudzi mwa Chituwawa, T/A Nthiramanja, Bright Eferemu, wa zaka 17, wa mmudzi mwa Soza ku T/A Njema onse a m’boma la Mulanje pomwe Christopher Jeke wazaka 19 amachokera m’mudzi mwa Kalinde kwa T/A Kaduya ku Phalombe ndi Manuel Juwawo wa zaka 23 ochokera ku Villa Milanje ku Mozambique.

Advertisement