Mtsogoleri wa dziko la Malawi a Lazarus Chakwera wati anthu ena akufuna kuti iye akhale ndi mphavu zonse pa ntchito za m’boma zomwe wati ndikusemphana ndi malamulo.
A Chakwera anena izi Lolemba pa 12 June, 2023 pomwe amatsekulira msonkhano wa masiku awiri wokhudza kulekanitsidwa kwa mphamvu za ulamuliro womwe ukuchitikira ku Bingu International Convention Centre (BICC) mumzinda wa Lilongwe.
Polankhula pa msonkhanowo, a Chakwera anadabwa kuti n’chifukwa chiyani anthu ochuluka m’Malawi muno amafuna kuti iwo azilamulira dziko lino monga mmene zinkakhalira pa nthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi.
A Chakwera ati izi zikusonyeza kuti anthu ambiri sadziwa ntchito za pulezidenti komanso kulekana kwa mphavu za ulamuliro monga momwe zinakhazikitsidwira m’malamulo oyendetsera dziko lino, koma anenetsa kuti iwo apitiliza kusunga ndi kuteteza malamulo a dziko lino.
“Nanga sikale timaimba kuti zonse ndi za Kamuzu. Ndiye chifukwa tinazolowera zina zotelezo, chili chose timangofuna olamula akhale pulezidenti koma malamulo tinasintha, tinaika malamulo akuti angakhale pulezidenti aziyankha osati kungolamula ayi.
“Pulezidenti si chauta. Chauta ndiyekhayo amene ndi ogamula, opeleka malamulo komaso ndamene ali ndi mphavu zonse osati wina aliyese waife, ndipo palibe pakati pathu amene akuyenera kukhala ndi mphavu zonse,” atelo a Chakwera.
A Chakwera anapitilira ndikuyelekeza ntchito ya mtsogoleri wa dziko ndiwa polisi wa pansewu yemwe anati amakhala ndi mphavu zongolamulira kayendedwe kabwino ka pansewu koma samakhala ndi ulamuliro onse pa magalimoto.
“Tsiku ndi tsiku, anthu amayelekeza kuyendetsa boma ndi fanizo la dalaivala yemwe ali ndi mphamvu zonse pa makina. Koma zoona zake mzakuti ntchito za mtsogoleri wadziko zimafanana ndi wa polisi wa pansewu amene amalamura kayendedwe ka magalimoto pansewu koma alibe mphavu zonse pa magalimotowo,” anaonjezera choncho a Chakwera.
Mtsogoleri wa dziko linoyu adatinso nzika zikuyenera kumafusa atsogoleri onse a nthambi zitatu za boma zomwe ndikuphatikizapo ma ofesi a mtsogoleri wa dziko, mabwalo oweruza milandu komaso nyumba ya malamulo omwe wati anapatsidwa udindo wogwiritsa ntchito mphamvu za boma.
A Chakwera adaululanso kuti kangapo konse alandira mafoni kuchokera kwa anthu osiyanasiyana omwe ati amawakakamiza iwo kuchita zinthu zophwanya malamulo ndipo adati anthu enaso amawalimbikitsa kuti athane ndi aliyense amene akuwanyoza kapena kuyankhula zotsutsana ndi mfundo za boma lawo.
“Ndiye palinso ena amene amafuna kundiopseza chifukwa choti sakugwirizana ndi mfundo za boma zomwe ndikudziwa kuti ndi zopindulira dziko lino, ngati sadziwa kuti ndinapanga lumbiro logwira ntchito za ofesi yanga mopanda mantha.
“Ndiye palinso ena amene amandilangiza kuti ndigwiritse ntchito mphamvu za ofesi yanga pothana ndi anthu amene amandidzudzula kapena kundilankhula zoipa komanso kupereka mphoto kwa amene amandikometsera ngati sanandimve ndikulumbira zaka zitatu zapitazo kuti ndizakwaniritsa ntchito za ofesi yanga popanda maganizo oyipa,” anawonjezera choncho a Chakwera.
A Chakwera ati ali ndi chiyembekezo choti msonkhanowu uthandiza kuphunzitsa anthu kudziwa malire a mphavu za mtsogoleri wa dziko komaso kusiyana kwa mphavu za ulamuliro m’nthambi za boma.
Msonkhanowu omwe ukuyembekezeka kutha lero lachiwiri, ukutsogoleledwa ndi atsogoleri a nthambi zitatu za boma, omwe ndi a Chakwera monga mkulu wa akuluakulu a boma, Chief Justice Rezine Mzikamanda monga mkulu wa zamalamulo, komanso sipikala wa nyumba ya malamulo Catherine Gotani Hara monga mkulu wa nyumba ya malamulo.
Follow us on Twitter: