M’khalakale pamaimbidwe Peter Sambo wati chamba cha lege chomwe wayamba kuyimba pano, chimuthandiza kuti afikile anthu ochuluka ndi uthenga wabwino kuposa momwe amayimba nyimbo zauzimu.
Nkhaniyi ikutsatira kubwera poyera kwa oyimbayu ndikulengeza kuti kuyambira tsopano sadziyimba nyimbo zauzimu zokhazokha pomwe wakhazikitsa chamba chake chatsopano chomwe akuchitchula kuti ‘Afro-reggae’.
Sambo wati ngakhale kuti kuyambira pano sakhazikika pakuyimba nyimbo zauzimu zokhazokha, iye aziyimba nyimbo zomwe zidzikhala ndi uthenga wabwino mu chamba cha lege.
Potsatira izi anthu m’masamba a mchezo anatanthauzira uthengawu ngati kuti Sambo wasiyilatu kuyimba nyimbo zauzimu zomwe mwini wake wakana kuti sichoncho.
Sambo mkati mwa sabatayi analemba patsamba lake la fesibuku kufotokoza mwachimvemve tanthauzo la zomwe wachita pokhazikitsa chamba chake cha ‘Afro-reggae’.
Iye wati kuyimba nyimbo zauzimu zokha monga wakhala akupangira mmbuyomu, zakhala zikumupangitsa kuti asakwanitse kufikira magulu ena a anthu ndi uthenga wabwino omwe nyimbo zake zimanyamula.
Sambo yemwe anatchuka kwambiri ndi nyimbo ya ‘Tachilowa’, wati akuona kuti pano akhala omasuka kuyimba nyimbo zomwe zinyamule uthenga wa mtendere ndi chikondi muchamba cha lege (reggae) chomwe akuti chili m’magazi mwake.
“Ndine woyimba ndipo nyimbo zauzimu ndizomwe ndimakonda komanso ndiye mayitanidwe anga, koma nyimbo zimaposa chipembedzo ndi chikhulupiriro.
“Ndazindikira kuti nditha kutumikira ntchito yanga bwino popanga mtundu wanyimbo womwe nditha kufalitsa bwino uthenga wanga wa chikondi, umodzi ndi mgwirizano, ndipo ndichifukwa chake ndidapanga nyimbo za Afro-reggae,” watelo Sambo.
Mkati mwa sabata yomweyi, Sambo anauzaso imodzi mwa nyumba zofalitsira uthenga m’dziko muno kuti vuto ndiloti anthu nyimbo zauzimu amazitenga ngati chamba pachokha zomwe wati sizili choncho ponena kuti nyimbo zauzimu ndiuthenga chabe.
“Ndine woyimba ndipo luso langa limaposa chipembedzo ndi chikhulupiliro, ndikufuna kuchita zomwe ndikudziwa bwino, reggae chakhala chamba cha kumtima kwanga kuyambira pamene ndinabadwa.
“Tsopano ndikufuna kuti ndifikile anthu amitundu yochuluka. Nyimbo zauzimu sizimakwanitsa kuthana ndi mavuto ena okhudza mitundu ndi chikhalidwe cha anthu,” anateloso Sambo.
Sambo walonjeza kuti kusintha kwake pamayimbidwe sakhumudwitsa nako anthu omutsata ndipo wati anthu ayembekeze nyimbo za reggae ya chiAfrica zapamwamba.
Pakadali pano anthu ena amuyamikira oyimbayu kaamba kachiganizo chake choyamba kuyimba nyimbo za chamba cha lege, pamene ena akumudzudzula ponena kuti wakhala ngati Agalatiya opusa, oyamba ndi zabwino kutsiliza ndi zoyipa.
Katswiriyu akuyembekezeka kukhazikitsa chimbale chotchedwa ‘Zakumwamba’ mkatikati mwa chaka chino mumzinda wa Lilongwe.
Zina mwa nyimbo zomwe zili muchimbale chatsopanochi ndi monga ‘Amamaliza’ yomwe waimba ndi Saxess, ‘Ndamuyesa Yesu’ yomwe waimbandi Allan Chirwa komaso ‘Thandizo’ yomwe waimba ndi Lulu.
Follow us on Twitter: