Monga malemu John ‘Izeki’ Nyanga ananena kale kuti “zina umangoona waziyamba,” panza Yassin ‘Ichocho’ Suwedi wachimina ndipo akuziguguda pachifuwa uku akuyankhula yekha yekha kuti kodi moyowu unkalinda kuteleku? Panzayu apempha anduna kuti amukhululukile.
Potsatira zomwe nduna ya zachitetezo a Ken Zikhale Ng’oma analamula kuti kampani ya Ichocho Power Security (IPS) ilandidwe chiphaso, mwini wake wa kampaniyi Ichocho Suwedi watulutsaso kalata yopepesa.
A Zikhale Ng’oma analamula izi kaamba ka kusaweluzika kwa Ichocho yemwe posachedwapa anatulutsa kanema yomuuza namandwa poyimira anthu pa milandu a Jai Banda kuti mwana wawo Tonderai wagwidwa ndi gulu lawo la IPS ndipo likumusunga ngati kapolo.
Ichocho anauza a Banda kuti adzamuonaso mwana wawo Tonderai pokhapokha avomele kuyimilira gulu lake pa pempho lawo lopita ku boma kuti gululi lizitengedwa ngati gulu la asilikari a nkhondo a dziko lino.
Izi zinakwiyitsa anthu ochuluka mdziko muno kuphatikizapo a nduna a Zikhale Ng’oma omwe analamula kuti kampaniyi ilandidwe chiphaso chake.
Komatu ngakhale Ichocho Suwedi mkati mwa sabatayi anatulutsa kale kanema ina yopepesa kaamba ka zomwe anayankhulazi, mkuluyu wapepesaso.
Ichocho Suwedi walemba kalata yomwe ikupita kwa anduna a Zikhale Ng’oma yopempha chikhululukilo ndipo wanenetsa kuti wachimina ndipo sadzayambilaso.
Mukalatayi chiphonachi chabweleza kunena kuti zomwe chinayankhula mu kanema yo zinali nthabwala chabe ndipo sizinachitike.
“Potsatila malangizo omwe ndakhala ndikulandira kuchokera kwa anthu osiyanasiyana kuphatikiza ofesi yanu, ndine wa chisoni kwambiri chifukwa cha zomwe mnayankhula. Ndinaphunzira kuti zochita zanga zadzetsa mantha kwa a Malawi ngati kuti ndine wakuba anthu komaso zayika chitetezo cha dziko lino pachiswe.
“Choncho ndikupepesa chifukwa cha kanema yomwe ndidayika patsamba la nchezo momwe muli uthenga wowopseza. Ndikufuna nditsimikizire ofesi yanu yabwino kuti khalidwe loipa lotere komanso kulankhula mosasamala kwantundu uwu sizidzachitikanso mtsogolomu,” wapepesa choncho Ichocho mu kalata yake.