Kalindo adzudzulidwa kamba kofuna kuti Chizuma achotsedwe ntchito

Advertisement
Bon Kalindo

Anthu ena m’dziko muno akupitilira kudzudzula zomwe wayankhula Bon Kalindo posachedwapa kuti mkulu wa bungwe lothana ndi katangale la ACB, a Martha Chizuma, achotsedwe ntchito.

Nkhaniyi ikudza pomwe posachedwapa bwalo la milandu mu mzinda wa Mzuzu mwezi uno lalamura kuti apolisi afufuze nkhani yoti a Chizuma anauza munthu wina zinsinsi za ntchito yawo zomwe samayenera kuwuwulura.

Potsatira izi a Kalindo omwe omwe miyezi yapitayi akhala akuchititsa zionetsero zosakondwa ndi boma la Tonse, ati ndikwabwino kuti a Chizuma ayambe ayima kaye ntchito yawo ngati mkulu wa ACB kufikila khothi lizamalize kufufuza nkhani yomwe iwo akufufuzidwa.

Malingana ndi mkuluyu, kuyimitsa pa ntchito a Chizuma, kuthandiza kuti kafukufuku wa apolisi pa nkhaniyi ayende bwino ndikuti chilungamo pa milandu omwe akuwaganizira owulura zisisi za ntchito yawo, chiwoneke.

Iwo apeleka masiku asanu ndi awiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti achotse a Chizuma ndipo ati ngati izi sizichitika m’masikuwa, iwo apita ku msewu kukachita zionetsero mpaka a Chizuma atachotsedwa.

“Iwowo atule pansi udindo ndicholinga choti afufuzidwe pa nkhani zimene akhothi anagamula kuti zichitike,” atelo a Kalindo.

Ndipo pothilira ndemanga pa zankhaniyi, m’modzi mwa anthu olimbikitsa kuthana ndi katangale omweso amayimilira anthu pamilandu a Sylvester Ayuba James, ati maganizo a Kalindo ndiwolakwika kwambiri.

Ayuba James yemwe amayankhula ndi imodzi mwa nyumba zofalitsira mau mdziko muno, ati a Kalindo sakudziwa chenicheni chomwe akufuna atakwanilitsa.

“A Kalindo akundionekera ngati munthu osokonekera, osadziwa chomwe akuchita komaso chomwe akuyenera kutsata pa malamuro. Kusokonekera uku ndikunena makamaka pa nkhani ya malamuro kuti iwo sakuzitsata,” watelo Ayuba James.

Nawo a Mustapher Hussein omwe ndikatswiri pandale, ati ganizoli ndilosayenera zomweso ati zitha kuchedwetsa ntchito yothana ndi katangale ndipo ati a Chizuma sangachotsedwe ntchito kaamba koti a Kalindo aopseza kuti achita zionetsero.

A George Chaima omweso ndikatswiri pankhani za ndale, anaonjezera kuti; “Ndizodabwitsa m’mene iwowo akupangira. Pena zikuoneka kuti a Kalindo akumadzitsutsa okha, Pena akulankhula ngati za nzeru, nde mwina nkovuta nthawi zina kuzitenga zomwe akulankhura a Kalindo,”

A Malawi enaso omwe amathilira ndemanga pankhaniyi makamaka m’masamba a mchezo osiyanasiyana, ati akuganiza kuti a Kalindo adyetsedwa banzi ndi anthu omwe akuganizilidwa kuti anachita katangale.

Advertisement