Kampani yogulitsa magetsi mdziko muno ya Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM) yatsutsa mwantu wagalu mphekesera yomwe ikumveka yoti ikufuna kukweza mtengo wa magetsi.
Nkhaniyi ikutsatira mphekesera yomwe yakhala ikuveka kuyambira kumayambiliro kwa sabata ino pomwe akuti kampaniyi ili ndi dongosolo loti kumayambiliro kwa mwezi wamawa, mtengo wa magetsi uwonjezeredwe.
Malipoti omwe anthu akhala akugawana makamaka pamasamba a mchezo ndiwoti ESCOM yalembera kalata bungwe loyang’anira za mphamvu la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) kilidziwitsa zamalingaliro ofuno kukweza mtengo wa magetsiwu.
Koma ngakhale zili choncho, mmodzi mwa akuluakulu ESCOM akana mphekeserayi ponena kuti ndibodza lamkunkhuniza.
Malingana ndi ofalitsa nkhani ku kampani ya ESCOM a Innocent Chitosi, zomwe nyumba zina zofalitsa nkhani zinaulutsa mkati mwasabatayi pankhaniyi, ndizabodza.
“Sizowona kuti ku ESCOM talembera kalata bungwe lowona za mphamvu la MERA kuti litilole kuti tikweze mtengo wa magetsi. Anthu asadere nkhawa zankhaniyi, ili ndi bodza,” atelo a Chitosi.
Nkhaniyi ikubwera pomweso bungwe la MERA latsimikiza kuti mitengo yogulira mafuta agalimoto ikhoza kukwera m’dziko muno kutsatira kukwera kwa mitengo yogulira mafutawa pa msika wa dziko lonse.
Mneneri wa MERA a Fitina Khonje awuza zina mwa nyumba zofalitsira nkhani m’dziko muno kuti zina mwa zifukwa zomwe mafutawa angathe kukwelera mtengo ndi kaamba koti ndalama ya dziko lino yakhala ikuchepa mphamvu pa msika wa kunja.