Nankhumwa, Grezelda ndi ena awiri awabwezeretsa mu DPP

Advertisement

Chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) chabwezeretsa akuluakulu anayi omwe chinawachotsa mu mchipanichi komaso pa maudindo awo kaamba kosasunga mwambo.

A Kondwani Nankhumwa omwe ndi mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakummwera, mlembi wa mkulu a Grezelda Jeffrey, msungichuma wamkulu a Jappie Mhango komaso a Yusuf Nthenda, anachotsedwa mchipanichi mwezi wa October chaka chatha.

Potsatira izi, anayiwa anakamang’ala kubwalo la milandu kutsutsana ndi chiganizochi ponena kuti iwo samagwirizana ndi zomwe akuluakulu a chipanichi amanena kuti iwo anaphwanya ena mwa malamulo a chipanichi.

Ndipo pamene nkhaniyi inali isanamalizidwe kuzengedwa kubwalo lamilandu, komiti yaikulu ya chipanichi yabweza ganizo lake lochotsa anayiwa m’maudindo awo komaso mchipanichi.

Malingana ndi chikalata chomwe chasainidwa ndi mlembi wa komitiyi a Francis Mphepo, ganizo lobwezeretsa anthuwa mchipanichi komanso m’maudindo awo labwera powona kuti anthuwa akabwelera mchipanichi adzatsatira malamulo onse.

“Komiti yaikulu yapanga ganizoli poganiza kuti mukabwelera mchipanimu komaso paudindo wanu ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani mchigawo chakummwera, mudzatsata malamulo achipani komaso mudzalemekeza utsogoleri wa chipani. Takulandiraniso ku DPP,” yatelo kalata yopita kwa a Nankhumwa.

Koma titawaimbira foni kuti timve mbali yawo pankhaniyi, a Nankhumwa ati pakadali pano kalatayi siyinawafike ndipo ati akufuna akayambe ayang’ana kaye ku ofesi kwawo ngatidi yafika.

Iwo anati pakadali pano sangathe kukamba zambiri kaamba koti sakudziwa kuti kalatayi yanyamula uthenga otani.

Advertisement

6 Comments

Comments are closed.