Chilima ankafuna kubwelera ku DPP, Mutharika anakana powopa kuphedwa – Nankhumwa

Advertisement
Chilima Malawi Vice President Missing

Mtsogoleri wa chipani cha People’s Development (PDP), Kondwani Nankhumwa, wati mu 2019, malemu Saulos Chilima ankafuna kuthetsa mlandu wa chisankho ndikubwelera ku chipani cha Democratic Progressive (DPP), koma a Peter Mutharika anakana powopa kuti awapha ndikutenga udindo wawo.

Nankhumwa wanena izi Lamulungu madzulo pomwe amacheza ndi wayilesi ya Zodiak mu pologalamu yapadera momwe wati Chilima anawatuma iwo kuti akawapemphere kwa Mutharika kuti akumane ndikukambirana zokhudza kubweleraso ku chipani cha DPP.

Nankhumwa wati a Chilima anawaitanitsa ndikuwauza kuti zionetsero zomwe zimachitika nthawi imeneyo (2019), sizimawasangalatsa, ndipo anawatuma kuti akawapemphere kwa a Mutharika kuti akumane akambirane.

Kondwani Nankhumwa
Nankhumwa: anthu amatha kukudetsa.

“Ine ndinatenga uthenga ndikukauza a Mutharika ndipo anati amva, koma anandibweza kuti ndikamuuze kuti iwo akumana naye pokhapokha (Chilima-yo) athetse mlandu wa zisankho omwe unali kukhothi komaso adzudzule zionetsero zomwe zinkachitika nthawi imene ija kudzera pa nsonkhano wa atolankhani,” watelo Nankhumwa.

Nankhumwa wati m’malo mwake, Chilima anenena kuti iwo angochepetsa mboni pa mlandu wa chisankho osati kuwuthetsa komaso anadzipeleka kuti asiya kupezeka ku zionetsero zomwe a Mutharika anagwirizana nazo.

Ngakhale kuti a Chilima anapanga zonsezi kuti maloto awo ofuna kubweleraso ku DPP akwanilitsidwe, a Mutharika sanakumanebe ndi malemuwa ngakhale kuti anakumbutsidwa kangapo konse.

A Nankhumwa ati, “Chilima ankafusabe zoti akumane zija, koma kumapeto kwake a Mutharika anakana ponena kuti akakumana ndi Chilima atha kuphedwa ngati momwe anaphedwera Bingu wa Mutharika. Iwo anatiso amva kuti Chilima akufuna awaphe kuti akhale pulezidenti kenaka andisankhe ine (Nankhumwa) kuti ndikhale wachiwiri wake.”

Iwo ati afotokoza izi pano pofuna kutsindika kuti nthawi zina anthu amatha kukudetsa pamene ndiwe oyera komaso pena anthu amatha kukuyeretsa pamene ndiwe wakuda.

Chilima yemwe anafa pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu pangozi ya ndege pa 10 June chaka chino, adachoka ku DPP ndikukayambitsa chipani chake cha United Transformation Movement (UTM) mu 2018.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.