Aphunzitsi awopseza kuti ayambilaso sitalaka

Advertisement

Aphunzitsi m’dziko muno awopseza kuti ayambilaso kunyanyala ntchito ngati kwa masiku asanu ndi awiri (7) akubwerawa boma silipanga zomwe anagwirizana kumayambiliro kwa mwezi uno.

Pa 8 March chaka chino boma kudzera ku unduna wazamaphunziro linagwirizana ndi aphunzitsi kudzera Ku bungwe la TUM kuti liwapatsa aphunzitsiwa ndalama yoti aliyese akagule zozitetezera kumatenda a covid-19 zomwe ankati zikuimilira ndalama ya ukaziotche yomwe aphunzitsiwa ankafuna.

Mbali ziwirizi zinagwirizana kuti ndalamazi zipelekedwa kwa aphunzitsi pakutha pa masabata awiri zomwe mpaka lero sizinachitike ndipo pambuyo pake boma lamenyetsaso nkhwangwa pamwala kuti silipelekaso ndalama zomwe anagwirizanazi.

Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga mchakuti lachitatu pa 24 March, wapambando wakomiti ya zamaphunziro Ku nyumba ya malamulo a Brainnex Kaise alembera kalata bungwe la TUM kuti aphunzitsi ayiwale zolandira ndalama zomwe anagwilizanazi.

Malingana ndi a Kaise, chiganizochi chadza kaamba koti komiti ya mtsogoleri wa dziko yotsogolera ntchito yolimbana ndi covid-19 yakana mwantu wagalu kuti sizitheka kuti aphunzitsi apatsidwe ndalama zogulira zipangizo zozitetezelazi.

Poyankhapo zankhaniyi, bungwe la TUM kudzera kwa wapampando wake a Willie Malimba lati ndizokhumudwitsa kuti boma lasankha kuphwanya pangano lomwe anagwirizana masabata awiri apitawa.

Apa bungweli lalembera kalata boma komaso mbali zonse zokhudzidwa kuwadziwitsa kuti aphunzitsi onse msukulu za boma ayambilaso kunyanyala ntchito ngati boma silikwanitsa pangano lomwe anagwirizanali.

Chikalatachi chomwe asayinira ndi a Malimba, chapeleka masiku asanu ndi awiri (7) kuti boma lichitepo kanthu ndiposo chati sitalakayi ikayamba idzatha pokhapokha boma lidzapeleke ndalama zomwe anagwirizanazi kwa aphunzitsi onse.

“Poyang’ana chiganizo chomwe boma lapanga, ife tikupeleka masiku asanu ndi awiri (7) olidziwitsa boma kuti tikuyambilaso sitalaka yathu yomwe tinaiyimitsa kaamba kazokambilana komaso mgwirizano womwe tinapanga pa 8 March.

“Ife tikulichenjeza boma kuti Ulendo uno sitalakayi ikayamba idzatha pokhapokha aphunzitsi msukulu zaboma za primary, secondary komaso aphunzitsi a mma TTC akadzapatsidwa ndalama zogulira zozitetezera ku Covid-19 za miyezi itatu monga momwe tinagwirizanirana,” chatelo chikalata cha TUM.

Bungweli latiso ndilokonzeka kukambirana ngati boma komaso mbali zonse zokhudzidwa zingafune kutelo.

Advertisement