Ena akuti ikumveka ngati ya ma kadi ija a Malawi anaikana pa dzana mu ulamulilo wa Kongeresi. Ena akuti tisakambilane iyiyi pamene tikukanika kulimbana ndi katangale. Otakasika ena akutsindikanso kuti imeneyi ibwele ndithu, pasakhale munthu ongolandila mankhwala a ulere, ka wani pini ndi kachani.
Lingalilo la nyumba ya malamulo loti m’Malawi aliyense azipeleka 1 sauzande ya za umoyo pachaka lautsa mpungwepungwe pakati pa a Malawi amene akudandaula kuti boma likupakula kwambili.
Nthambi ya nyumba ya malamulo yoona za umoyo inanena kuti zikufunika kuti boma liyambe kutolela ka chamwaka kwa a Malawi onse pa chaka kuti azithandizapo pa ntchito za umoyo. Malinga ndi mtsogoleri wa nthambi’yi, a Matthews Ngwale, bajeti ya za umoyo ya dziko lino ikupwetekeka kambili Kamba koti si a Malawi onse amene amatengapo gawo posonkha ku gawoli.
“Titati pa chaka, munthu aliyense azipeleka ka 1 sauzande, zitha kusintha zinthu,” anatelo a Ngwale.
Lingalilo la a Ngwale limene ena, kuphatikizapo katakwe pa zachuma ndi malonda a Henry Kachaje, analilandila ndi manja awiri lakhumudwitsa a Malawi ena amene ananena kuti sakumvetsa kuti cholinga cha ka pini kameneka ndi chani.
“Kodi apa sindiye kuti tikuyambilanso kukhoma ma khadi tinawakana pa dzana aja?” anafunsa modabwa choncho mkulu wina pa makina a mchezo a Facebook pamene nkhaniyi inakambidwa.
Nkhani ya ma khadi ndi imodzi mwa nkhani zimene zinapangitsa a Malawi kukwiyila chipani cha Kongeresi ndi kuchichotsa mu boma mu chaka cha 1994. Pano, asanathe chaka ndi komwe mu boma, ena akuyesa ngati aibweletsanso nkhani imeneyi.
Koma ena atsutsa lingaliloli ati Kamba koti silikuthana ndi vuto lenileni.
“A Malawi timapeleka misonkho yochuluka imene imangothela m’thumba mwa anthu, nkhani apa si yoti tipeleke ndalama zina, musoke matumba obookawo osati kumangotoitchaja ife ayi,” anatelo m’Malawi wina osakondwa ndi ganizoli.
Amene akuyima pa mbali imeneyi akuona kuti vuto si ndalama zopita ku umoyo, ndi kagwilitsidwe ka ntchito ka ndalamazo.
Koma ena akuona kuti 1 sauzande ndi ndalama yochepa yomwe anthu angathe kupeleka pa umoyo wawo.
“Umoyo n’kutengulila, ka 1 sauzande kokha kuti mupeze chithandizo kuchipatala koma kudandaula? Mwazolowela zaulele udyo,” anatelo ena.