Covid: aletsa mowa ku Joweni, odwala afika 1 miliyoni, a Malawi ochuluka akubwelelako

Advertisement

Nthenda yatisautsa mu chaka chino ya Covid yaluma mano ndi kupana mu dziko la South Africa kumene a Malawi ochuluka akubwelelako sabata ndi sabata.

Malingana ndi malipoti ochokela mu dzikolo, anthu okwana 1 miliyoni tsopano ndi amene adwalako nthendayi mu chakacha. Dzulo lolemba pa 28 Disembala, mtsogoleri wa dziko la South Africa a Cyril Ramaphosa analengeza kuti akutseka dzikolo Kamba ka matendawa.

“Tikubwelelanso ku nyengo zowawitsa zija,” anatelo a Ramaphosa. “Kuyambila 9 koloko usiku mpaka 6 koloko mammawa, pasapezekenso munthu akuyendayenda mu dziko muno popanda chifukwa chenicheni.”

Iwonso analengeza kuti kagulitsidwe ndi kamwedwe ka mowa mu dziko’mo kakhala ndi malile tsopano. Analamulanso kuti anthu mu dzikomo azivala zozitchingila ku nkhope ndipo olephela kutelo azimangidwa kwa miyezi isanu ndi umodzi (6) kapena kupeleka chindapusa, ena azipeleka chindapusa andi kumangidwanso ngati banyila.

Mu dziko la South Africa ati mwapezeka matenda a Covid-19 oopsa amene akufalitsidwa mwachangu, kudza ndi ukali komanso kugwila achinyamata limodzi ndi akulu omwe.

Pamene izi zili chonchi, a Malawi ochuluka akubwelela kuchoka mu dziko la South Africa maka pothawa mavuto a za chuma ndi kusowa ntchito amene mliri wa coronavirus wabweletsa mu dzikolo.

Ambili akubwela pa bus ndipo sakuyezedwa moyenela asanakwele bus. Ena akafika mu dziko muno sakukwanitsa ndi komwe kuzipatula kwa sabata ziwili monga akuyenela munthu amene wachoka mu dziko limene mliri wa coronavirus waluma mano.

Advertisement