Phungu wa DPP wapezeka ndi Coronavirus

...chiwelengero chaopezeka ndi kachiromboka chafika pa 1818

Malawi24.com

Phungu wa chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP) wapezeka ndi kachirombo ka Corona komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19.

Izi ndimalingana ndi phunguyu, a yemwe analembera anzake komaso achibale ake kuwadziwitsa za nkhaniyi.

Olemekezeka a Chione Mwase a ku mvuma kwa boma la NkhataBay omwe ndi phungu oyamba kupezeka ndi nthenda ya COVID-19 mdziko lino ati pakadali pano awagoneka pa chipatala cha Queen Elizabeth Central ku Blantyre komwe akulandira thandizo.

Iwo apempha achibale komaso anzawo onse kuti aziwapemphelera komaso apempha aphungu anyumba yamalamulo omwe anakumana nawo posachedwapa kuti nawoso akayezetse kuti adziwe ngati ali ndi nthendayi.

“Ndafuna ndikudziwitseni kuti ndapezeka ndikachirombo ka Corona ndipo ndagonekedwa pachipatala cha Queen Elizabeth. Muzindipemphelera, ndipo ngati ndingamwalire tikaonana kumwamba.

“Ndimakukondani nonse aphungu anyumba yamalamulo, komaso ndikukupemphani samalani ndi nthendayi. Kwanose amene tinakumana kunyumba yamalamulo posachedwapa chonde pitani akakuyezeni musachedwe,” anatero a Chione Mwase.

Potsatira nkhaniyi, wapampando wa komiti ya mtsogoleri wadziko yolimbana ndi mlili wa COVID-19, Dr John Phuka wati wakumana kale ndi komiti yoyendesa ntchito za nyumba ya malamulo pa nkhaniyi.

Pakadali pano a Malawi ena okwana 76 apezekaso ndikachirombo ka Corona mumaola 24 apitawa ngakhale kuti palibe yemwe chachira kapena kumwaliraso ndinthendayi.

Mwaomwe apezekawa, 31 ndiochokera ku Mzuzu, 18 ochokera ku Lilongwe, 15 ku Blantyre, pamene mmaboma a Mzimba ndi Mchinji kwapezeka anayi anayi ndipo atatu apezeka m’boma la Mwanza pamene ku Karonga kwapezeka m’modzi.

Izi zapangitsa kuti chiwelengero chaomwe apezeka ndikachiromboka chifike pa 1818 tsopano pomwe anthu 19 ndiomwe amwalira ndinthendayi ndipo anthu 317 ndiomwe achira zomwe zikutanthauza kuti anthu 1484 ndiomwe akudwalabe nthendayi pakadali pano.

Advertisement