A Mutharika akufuna aphe ine ndi Chakwera — Chilima

...atinso akufuna kupha a Mtambo ndi Trapence

Zina ukamva, mutu mpaka kupweteka mwa ching’alang’ala.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima walengeza kuti akudziwa za upandu umene boma la a Mutharika likukonzekela kuchita pa moyo wawo.

A Chilima amene tsopano asiya zofuna utsogoleri wa dziko lino ndi kuima ngati wachiwili wa a Chakwera pa chisankho cha pa 2 Julaye ananena izi mu mzinda wa Lilongwe pa maliro.

Iwo anati pa mkumano wa nduna za boma la a Mutharika lachinayi la sabata latha kunakambidwa zoti boma lipeze njira zowaphela iwo ndi cholinga choti masankho alepheleke.

“Ndipo si ine ndekha akufuna kumupha, akufunanso kupha a Chakwera,” a Chilima anatelo.

Ndipo iwo anaonjezelapo kuti boma la a Mutharika likufunanso kupha mtsogoleri wa bungwe la HRDC, a Gift Trapence komanso amene ankatsogolera HRDC pa dzana, a Timothy Mtambo.

A Mtambo nawo anakambapo kuti boma la DPP lakhala likufuna asing’anga kuti liwaphe mumatsenga koma lawakanika.

Advertisement