Pamene anthu m’dziko muno ali tcheru kudikira chigamulo kuchokera ku khoti pa mlandu wa zotsatira za chisankho cha mtsogoleri was dziko lino, akazembe a m’maiko osiyanasiya kuno ku Malawi apempha atsogoleri a ndale kuti azavomereze chigamulochi.
Akazembe a m’maiko monga United States, Unted Kingdom, Japan komanso Norway, Germany ndi Ireland ndi ena mwa akazembe omwe atulutsa chikalatachi.
Iwo ati akudziwa zoti anthu akukhala a mantha komanso a chidwi poyembekedza zotsatira za mlandu okhudza zotsatira za chisankho cha pulezidenti chomwe chinachitika chaka chatha.
Muchikalata chawo, akazembewa ati ali ndi chiyembekezo chachikulu choti a Malawi akhala akutsata malamulo komanso kulemekedza ufulu omwe iwo alinao.
“Panthawi yovuta ngati iyi mu mbiri ya dziko la Malawi, tikupempha mbali zonse zodandaula komanso zodandaulidwa, zipani zandale komanso otsatira zipanizo, komanso aMalawi ena onse posatengera chipani chomwe amatsata kuti alemekeze chiganizo chakhoti pa mlanduwu ndipo kwa omwe mlanduwu suwakomera, atsate njira zoyenela pofuna kupitiliza mlanduwu,” chatero chikalatacho.
Potengela kuti malamulo amalola anthu kupanga zioneselo, iwo apempha kuti anthu atha kutero koma mwabata ndi mtendere.
“Tikupempha anthu ayende mwamtendere komanso motsata malamulo. Okhwimitsa chitetezo akuyenela kupitiliza kuonetsetsa kuti bata ndi mtendere zikupitilira.”
Kuonjezera apo, atsogoleri azipani zosiyanasiyana apemphedwa kuti abwere pamodzi nkukambirana pofuna kudzetsa mtendere mdziko muno.
Mlanduwu ndi omwe a Dr. Saulosi Klaus Chilima omwe ndi a chipani cha UTM komanso Dr. Lazarus Chakwera a chipani cha MCP anakamang’ala kukhoti ponena kuti zisankhozi zomwe anapambana ndi a Peter Mutharika sizinayende bwino.
Chigamulo pa mlanduwu chikuyembekezeka kupelekedwa pa 3 February chaka chomwe chino.
Ndizomwe tikudikilila