Ati iwo adanena kale kuti dziko liri mmanja mwa agalu koma ena adali kukayika, tsopano pano ndi uthenga umene afuula Mayi Callista Mutharika mu chipululu kuti a Peter azitaye ndiye kuti zaphelezera basi.
Amene akutchulidwa kuti azakhala wachiwiri kwa a Chakwera pa chisankho cha 2019, a Sidik Mia ati kubwela poyera kwa Mayi Callista Mutharika ndi kunena kuti 2019 chipani cha DPP sichipambana ngati a Peter Mutharika ati ayimile ndi kugwilizana ndi zimene iwo ndi a Kongiresi akhala akukamba.
Polemba pa tsamba lawo la pa Facebook, a Mia ati kubwela poyela kwa a Callista ndi kuchenjeza anthu a chipani cha DPP komanso kutonza utsogoleri wa alamu awo nndi umboni oti mu dziko muno zinthu sizili bwino.
“A Mutharika ndi lebwedelebwede, ndipo kulephera kwawo kukuchita kuonekelatu,” analemba choncho a Mia.
Mwa zina, a Mia anatchulapo nkhani ya maphunziro a ku Yunivesite ndi kudandaula kuti boma la a Mutharika likulephela kuwalongosola. Iwo anafunsa kuti: “kodi maphunziro tsopano asanduka a anthu a chuma okha basi?”
Iwonso anakambapo nkhani ya kusowa ntchito ndi ya kuchepa kwa malipiro a anthu ogwila ntchito boma, zinthu zimene akuti zikuonetsa kuti a Mutharika akuvutika kulongosola boma.
Kanyimbi akugwirizana ndi zoti a Chilima azayimire DPP. Koma zoti malipilro m’boma akuchepa ndiye mmmmm ayi. Nkhani ndi yoti ogwira ntchito m’boma ambiri ndi a ulesi ndipo ndalama zomwe akulandira ndi zochuluka kwambiri poyerekeza ndi ntchito yomwe akugwira.
Mia iwe ndie ndindani mmmm
MIA ndiwe wabodza. Lebwedelebwede umatanthauza Msowoya osati Mutharika. Usanamize anthu