Tinanena kuti a Mutharika ndi lebwedelebwede, onani lero Callista wagwilizana nafe – Mia


sidik-mia-

Ati iwo adanena kale kuti dziko liri mmanja mwa agalu koma ena adali kukayika, tsopano pano ndi uthenga umene afuula Mayi Callista Mutharika mu chipululu kuti a Peter azitaye ndiye kuti zaphelezera basi.

Amene akutchulidwa kuti azakhala wachiwiri kwa a Chakwera pa chisankho cha 2019, a Sidik Mia ati kubwela poyera kwa Mayi Callista Mutharika ndi kunena kuti 2019 chipani cha DPP sichipambana ngati a Peter Mutharika ati ayimile ndi kugwilizana ndi zimene iwo ndi a Kongiresi akhala akukamba.

sidik-mia-
Mia: A Mutharika ndi lebwedelebwede.

Polemba pa tsamba lawo la pa Facebook, a Mia ati kubwela poyela kwa a Callista ndi kuchenjeza anthu a chipani cha DPP komanso kutonza utsogoleri wa alamu awo nndi umboni oti mu dziko muno zinthu sizili bwino.

“A Mutharika ndi lebwedelebwede, ndipo kulephera kwawo kukuchita kuonekelatu,” analemba choncho a Mia.

Mwa zina, a Mia anatchulapo nkhani ya maphunziro a ku Yunivesite ndi kudandaula kuti boma la a Mutharika likulephela kuwalongosola. Iwo anafunsa kuti: “kodi maphunziro tsopano asanduka a anthu a chuma okha basi?”

Iwonso anakambapo nkhani ya kusowa ntchito ndi ya kuchepa kwa malipiro a anthu ogwila ntchito boma, zinthu zimene akuti zikuonetsa kuti a Mutharika akuvutika kulongosola boma.

3 thoughts on “Tinanena kuti a Mutharika ndi lebwedelebwede, onani lero Callista wagwilizana nafe – Mia

  1. Kanyimbi akugwirizana ndi zoti a Chilima azayimire DPP. Koma zoti malipilro m’boma akuchepa ndiye mmmmm ayi. Nkhani ndi yoti ogwira ntchito m’boma ambiri ndi a ulesi ndipo ndalama zomwe akulandira ndi zochuluka kwambiri poyerekeza ndi ntchito yomwe akugwira.

  2. MIA ndiwe wabodza. Lebwedelebwede umatanthauza Msowoya osati Mutharika. Usanamize anthu

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading