A Malawi adzalipira pobwezeretsa chiphaso cha nzika – NRB

Advertisement
National ID Malawi

Nzika za dziko la Malawi zomwe zikhale ndi ziphaso za unzika zimene zili mkati mogawidwa mmadera ena zikuyenera kukonzeka mokwanira bwino pofuna kubwezeretsa ziphaso zawo zikazasiya kugwira ntchito kapena zikazasowa.

Malingana ndi mneneri wa bungwe loyendetsa za kalembera wa unzika mdziko muno a Norman Fulatila, poyankhula mu pulogalamu ya pa wailesi lachinayi ananenetsa kuti mzika za dziko lino zikalandira ziphaso zawo, zikuyenera kuzisamalira mokwanira bwino nthawi zonse.

norman-fulatira
Fulatira: Amalawi akuyenera kusamala ziphaso zawo.

Iwo anati kulembetsa mu kaundula wa unzika komwe nzika za dziko lino zalembetsa kunali kwa ulele ndipo atinso a Malawi akuyenera kulandiranso mwaulele osapereka kalikonse.

“Kugawa ziphasozi kudayambika kale mmadera omwe anayambilira kulembetsa ndipo kukupitilira koma mwa pang’ono-pang’ono, ziphasozi zikugawidwa mwaulele ndipo aliyense sakuyenera kupereka kanthu mcholinga choti atenge chiphaso chake, monganso m’mene anthu adalembetsera mwaulele koteronso kutenga,” analongosola Fulatira.

M’mau awo, a Fulatira anatsimikiza kuti ziphaso zikupitilira kufika mdziko muno pamene ziphaso za maboma ena anayi zafika mdziko muno ndipo zikuyembekezera kufika kwa eni ake m’malo momwe adalembetsera.

Iwo anati ziphaso za maboma a Dedza, Lilongwe, Ntcheu ndi Likoma zafika tsopano ndipo ziyamba kugawidwa pasadafike pa 1 December chaka chino.

Iwo anatinso ntchito yolongosola ziphaso mu ndondomeko yake ikumatenga masiku chifukwa zimabwera m’mulu umodzi.

Maboma omwe adali mu gawo loyamba mu kalembera wa dziko monga a Mchinji, Ntchisi, Salima, Nkhotakota, Dowa ndi  Kasungu adayamba kale kulandira ziphaso dzawo  kudzera mu mmalo amene adalembetsera.

A Fulatira anatinso a Malawi akuyenera kumatenga chizindikiro chowawonetsa kuti iwo ndi iwodi ndipo chiphaso ndi chawo, zinthu monga chipepala chomwe analembetsera, choyendetsera galimoto, choyendera mayiko a kunja ndi zina kuti athe kutenga chiphaso chawo, koma anatsimikiza kuti kutengerana chiphasochi nkosatheka.

Iwo anaonjezera kuti chiphaso cha unzikachi palibe munthu amene angapange cha chinyengo mu njira ina iliyonse popeza chili ndi zinthu zingapo zomwe ndi zovuta munthu kuzitsanzira nkupanga chiphaso chake.

“Nditsimikize pano kunena kuti palibe munthu amene angathe kupanga chiphaso chobera chifukwa chiphaso chathuchi chili ndi zitetezo zambiri zomwe ndi zovuta kubera, munthu oberayo ndekuti akuyenera kukhala ndi ma biliyoni a ma kwacha kuti abele komanso mzovutabe,” anaonjezera a Fulatira.

Gawo la chitatu kuyenera kulandira likhala la maboma a Blantyre, Chikwawa, Nsanje, Thyolo, Mulanje, ndi Chiradzulu omwe  adalinso mu gawo la chitatu  wa kalemberayu.

Advertisement

306 Comments

  1. Kumanda kuli ID? Tell me ! go to hell with your chiphaso cha nzika. Ndinabadwira momuno , Kamuzu, Bingu anafa sanali nzika? Zopanda ntchito ma IDs anuwo. Tikufuna mankhwala Ku chipatala not your card, you are after collecting money from poor pple. God is watching, mufa nazo nokha zimenezo.

  2. Za illuminati zomwezo mpaka expiry date nde kuti mukhala kuti pansi pa nyanja panu po mwapereka nsembe zingati a nrb koma ndikuuzeni a nrb sindimakuopani olo pangono ndili ndi yesu amene adzandi pulutse pakutha dzikoli bolani ndikachita bwino inu ba kwanili tsani malemba a boma nu a ndale nu a nrb zanu zimenezo.zakutha za dziko lapansi zimenezo.

  3. Book of life doesn’t expire until death stop stealing from your poor people. All SADC countries got unexpired Ids and u Malawi don’t u belong to SADC?

  4. Icant See Any Problem Here,nde Paja Amalawi Munazolowera Kuwawata,tie Nazoni,but To Me Ithnk Ths Is How Thngs Are Suppozd to be like.mwaiwala tmkadula #makadi? what pains me most is that iwas forced to buy a card 4 my #UNBORN BABY. hahaaa

  5. Ndinaziwa ine kuti boma ndi zomwe likazembera.even some of my freind can be my witnesses coz i once told them of this evil plan.nabola mzizatiganizila anthufe a kumudzi pa mitengo yakeyo.kma sizingandisangalase ngat nkhaniyi ndiyoona

  6. ngat akuziwa kut tonse tizilandira ndlama ndizosamuta koma moyo umene tili muno malawi ndiwau phawi ndiye sionse amene angakwanitse kulipira ndiye muyambe kae mwafusa anthu akumudz nzelu zawo

  7. kupanda kupanga renew azattan apa nde muzatmangatu olo muzatiuza kopita ndinu mesa anthu ankathawa zomwez ku MCP mukut inkadulitsta macard nw maso anu atseguka mufuna tibwererenso mbuyo ha ha ha ha nw i get our FUTURE IS THE PAST (UBULUTU TIZGANIZA POYAKHULA) tikadakodwa ikanakhala boma la MCP n tikanamvetsa

  8. kupanda kupanga renew azattan apa nde muzatmangatu olo muzatiuza kopita ndinu mesa anthu ankathawa zomwez ku MCP mukut inkadulitsta macard nw maso anu atseguka mufuna tibwererenso mbuyo ha ha ha ha nw i get our FUTURE IS THE PAST (UBULUTU TIZGANIZA POYAKHULA) tikadakodwa ikanakhala boma la MCP n tikanamvetsa

  9. So long as l know my home village,koma Boma la Malawi kubela anthu osauka lidzasiya liti and ndalama zomwe anthu azidzalipilazo zizidzapita kuti?Zipata za boma anthu anasumiya kupita amapita za private ndiponso kuli ma bank mkhonde anthu azipita kumeneko za lD zilibe ntchito kufuna kuba basi.Nanga abwanawo anapanga yawo?

  10. Funso nali; kodi chiphasocho chikatha ndekuti udzikawo uzitha mr dpp kapena tiziyenda mothawa ngati nthawi ya makadi ija civil war its wat wi want nw coz if peace fall apply force; udzika wabodzatu uwu chakwera sananame ayi

  11. Nkhuonapo vakufuntha pera mmalo wandeske makola Boma wize nanthowa zakulimbikitsa kut kwacha iwe nankhongono ndipo wakupangisha vima ID,,,vyaka vyakumanyuma takharanga uli kwambula viphasu ivo,,,ntchito mmalawi zikusowa ndipo wakupangisha viphasu kut vyachi

  12. Nde za manyi zimenezo! kodi nde kuti nonse mukumambirana zimenezi ku parliament ko ndinu ochokera ku UK!! zoona mzika yeni yeni ya ku Malawi angakhale akulankhula mbwelera ngati zimenezi yet akudziwa momwe malawi alili pano komanso kuchokera kale! Ndinu zitsiru za anthu nonse akunyumba ya Malamulo ko pa mtumbo panu mwandikwiitsa kwambiri. Anthu kumudzi akugona ndi njala chifukwa chosowa nchere weni weni ndithu nde muziti azikalipira manyi wanu wo! agalu inu matako anu

  13. Inu awa angotibela komadi ndi Malawi amenewa? At wuzuzebwi. Chomwe ndi kuziwa ine Malawis amaziwa uphawi ine sindizalipila. Akufuna ikhale ngati card ija? Kwakwana tatopa. Ifenso timafuna ndalama. Azalipile ndi amawo…

  14. chuma cha dziko lanthu mukugwetsa ndinu, koma mukufuna kutolera ma chenji kwa ife osaukisisa, ndichiti chinthu chosatha padziko lapasi? nde mkuti ikatha id iyo munthu azizaripira, munalakwisa nokha kuthamangisa chuma mu dzikomo

  15. ndipo ine ndikanabadwila dziko lina wosati malawi anthu wose akuluakulu mitu yinasiya kugwila wamoyo kulibe olopangono ntchito kuba kopanda nako manyazi munthu kulukulu basi dziko losauka kale kumabaso ndikanakhala fiti ndikana yambila iweyo wava please love you’re country

  16. kkkkkkk! amalawi osamapanga zinthu zoti simungakwanitse asiyileni aniake ma zambian chiphaso chabwanji chokhala ndi exp date ndikoyamba kuva ine uku…….ndizoseketsa kwa basi

  17. inu mumati katundu yense uja ma camera mpaka tinyumba tokhalamo pojambulitsa nzaulere? forsake muzilipira kumene zala za zikang’azo!!!!!

  18. Kkkkk,Malawi at 54,unzika uzikhala ndi expire?? I would love if they say those who will lose their IDs either through loss,damage or theft will be responsible for payments,I would have understood.Are we going back to party cards?

  19. Ine ndidzika ya dziko la Malawi kuchokera pachiyambi or ngakhale nditapanda kupanga chiphanso ichi,nzeru za nyapapi uyu nzakuba and adziwe kuti sitinkadziwa uyu or kumva za iye and sangaloze kuti anapangachinthu chotukula dziko la Malawi ali ku utchona wakewo and even panopa palibe development iliyonseyo ikuchitika chilowereni,kwake nkuba ndi azinzakewo chibwana,tionana 2019

  20. IDS have no expiry date, ask SA Home Affairs. Ikataika zoona umapeleka kangachepe. Unzika umachita expire? Zinazi tamafunsani abale.

  21. To my knowledge, ID does not expire like Passport, we have IDs here in South Africa but we don’t go and renew. What type of IDs re these ones? Is it ” Makhadi” like or what?

  22. What a waste of time….??? Ndie enafe kumachoka kutali ngati kunoku kuzapangisa ma ID..” kodi zomapangaso expire? Ohh no guys come on dis is unfair, hayyii aaaahh we learn through mistake

  23. Ine Chibwedzi Changa Chikukana Kugonana Titafusilana 2010 Mupaka Pano 2017 Chingakhale Chakodi Koma akukakamila kuti Ndisamusiye Chosecho Akuti Amayi Amaletsa Amomwe Kumakomelamo Wina Azikanila Kumatako Kwake Zachamba!!

  24. poyamba munapanga chiphaso chakuchipatala munthu akadwala… munayamba kuchigulisa K15 pano sindikuziwa kuti ndima sauzande angati koma muzipatalamo mulibe chithandizo chokwanila …bola inu mwapanga bizinesi ZAUMVE BASI

  25. Palibe kupanga lD kapena kulipira mungofuna kutibera ndalama bas ngat mulibe zopanga bola kungosiya vepiyo mmalo mokuti ukalimbane ndi magesi athu azikhala mowala uli busy kulimbana ndi athu

  26. koma amalawi mwachulukisa mabizinesi pa anthu osauka …koma palibe or chimodzi mukuchita chothandiza osauka …anthu akuchita kubalalikira maiko ena kuti mwina akamulawe tiyi …azisogoleri nonse manyazi mulibe

  27. Zikharanso ndi expiry bwanji ndekuti sizikansotu mpaka kulipilitsa mwationjeza kufuna kutibera kazipangani tikaonana kumwamba

  28. mmmmm kma ku malawi kumalemba apolice every yr kti azilanga akuba pamene mbanva ndinomwe .apolice gwirani ntchito yanu apa tione chifukwa mbanva zaoneka kale ndi izo za DPP iZo

  29. Do you believe there is a herbal doctor that cures HIV, I was positive for 9 years and Using ARVS , until I was cured completely by Dr. TIam, his herbal medicine is so strong and reliable. Call or WhatsApp him on : +2348037284837

  30. Inu monga boma plain inabwela ndiyinuyo ndiye chithu mwati ndichaulele ndiye choti tidzalipililanso ndichiyani? Nanga ngati munthu suna pangitse renew muzidzatani ? Mwachidziwikile muzidzayendanso mmakomo ndikumapanga check munthu osapangitsa renew muzidzamumanga like thawi yakamuzu . Mudzanyela inu timagona nazo mfutitu .

  31. Ndalama zanga ndizidzakumbira pansi, kuchipatala ndizidzapita kwa asing’anga, akakhala magetsi ndi solar. Ngati ndi fertilizer wama coupon akhale ndizidzalima soya. Kogula zovala ndiku free market. Akankhala madzi ndidzakumba chitsime. Kuchigayo sadzafuna ID. This is Africa not london kapena Australia. Asaaaaaa kumeneko kutseka njira ya anthu osauka kuti asapezebe bwino?

  32. Ploblem Ndinawona Wth Malawians Its We Behave Like Dzikoli Takabweleka Lathu Tasungixa Ndiye Tikuwononga Lobweleka Kenako Tikatenge Lathu…Issue Ya Id Siyachpani Ndi Policy Yokhazikika Meaning Chipani Chilichose Chizayendetsa Policy Yomweyo. Malawi Ali Ndi Njira Zochepa Zopeyela Ndalama Zoti Zitukule Malawi A Real Malawian Wil Nt Run From Renewal Coz We Want Change

  33. Kale kunali zodula ma card during kamuzu era, pano zabwerenso mwa ntundu wina,@list for replacement its ok to pay but not for renew

  34. Uku ndiye kuba anakuuzani ndi azingu okubawo kkkkkk ine ndizamwalila mmene analili abingu analibe ziphaso mapulani obela zisankho abwela kale koma kumalawi.eee njinga msonkho munthu akabeledwa osamu bwezela koma kkkk

  35. Nde mpaka id ya dziko kumakhala ndi expire date zokuba basi nde ikagwa ulipile dziko lokhala lako tiziliwopa Hahaha nde nthawi ya asamundatu hahahahahah ine mantha ndilibe without id

  36. Dont Forget That In Malawi Goverment Has A Diferent Way Of Finding Money,one Of It Is Bell Out From Police Station,people Are Taken To Police Station Without Proper Reasons So Right Now They Added Onother Way Of Gaining Money.

  37. U mzika ulibe expirely date bola akanati xikataika cox zidakwa nde azakhale ma customer .Nanga amene saxapangitsanso china chikaxapanga expire azatani naye

  38. Very unfortunate! Zoona adzalipire munthu akulephera kupeza ya mulu wa matemba kuti adye? Tiganizireni akakhala mavuto a zachuma popanga ziphasozi ife ngakhale mchere kuti tigule tikumakhala kuti taphupha malire mseru!

    1. Akunamatu amenewa ndani amene axakane kugulitsa munthu katundu woti akakhalitsa apanga expire kapena kuola iyaaa olo asatipasenso abasunga kameneko timaona ngati zanzeru

    2. Mukamakhala Ndi Mentality Ya Umphawi Simuzatukuka..Every Body Shud Contribute To The Development Of This Country..Stop Clapping Hands Fov Poverty

    3. Economy yathu ikhala bwanji bwino when our leaders are busy with their own pockets? Akukama yoonda kale yoti siikudya mkaka upezeka bwanji? People need to be empowered kawaoneni abale athu kumudzi mmene akuvutikira!

    4. Dziko Lake Liti Lopangila Chitukuko Ndalama Za Anthu Ovutika Akumudzi Kod Mwina Simuli Ku Malaw Konkuno Ma Cashgate Akupangika M’bomawa Simukuwaona? Boma Silingatukuke Ndi Ndalama Za A Amphawi
      Monga Inu Kukhala Mzika Wa Malawi Mudapangapo Expire? Mot Mudzizakanika Kuenda Pamseu Just Bcoz Your Id Yapanga Expire
      I Agree Wth You Mr Jabulan Mbewe

    5. We don’t like free things but we like affordable things! Do the government give us free things? Maybe u should remind me!

  39. Mwawonjeza 4yrs yokha basi chathakale chiphaso ndiye ife tizamwalira chamuma 2090 tikhala ndiziphaso zozaza nyumba bora naphili chikanatha 2030

  40. Makape, mufuna kutbela eti tizapanga athu achinyengo ngt kwa eni kuno zikutheka kuli bwanj kwathuko!! Ifenso tizakubereni Kod mukufuna kut muziba nokha??

  41. ziphaso za anthu ena zinasowa kodi nawonso ofunika adzalipilenso? Ndipo zinasowa eni ake asanazilandile. Komatu pamenepa ofunika tipaone bwino. tidzauzidwa kuti after election ziphaso zathu ndizopanda ntchito tikapangitsenso zina. Tiyeni tisamale a Malawi

  42. Identity Card ( ID) sikhala ndi Expire date ngati passport, chimenecho chimasonyeza unzika ndiye unzika umakhalanso expired date? Kikikikik basi apa zakanika Malawi akupita kuti? Ndizaulele komanso zosakhala expired date. Zili zonse kumangofuna kutolera ndalama kuchokera kwa mzika zomwe zili amphawi , inuyo mukungotenga ulele??hahahaha

  43. dziko la malawi ndilimodzi mwa maiko amu africa amene ali ndi njira zambiri zokhomelera nzika zake,ndinalakwa chani kuti ndi ndikhale m’malawi inee,amayiiineee!

  44. Expire date??,Iyi sipassport yokhala ndimalire.Inu uzikawuno uzikhala ndi Expire??,pa malawi tisamukapo eti??.Ooh tandiuzeni ngati munthu atalephera kulipira chikatha chipepala chaumzikachi,chosatira azikhala sim’malawi eti??.Malawi sazamva basi.Ayi mutifunira kokhala.

  45. That is total kak, what type of damn ID is that?.Tuzadulanako makosi kumeneko.Unzika ochita kugulitsanawo wamtundu wanji?.Kodi pakati pa DPP ndi anthufe amane akufuna ID ndindani?.
    Kubakotu muganize bwino.We don’t want blood in future.

    1. thamie sukuona or kumva ai kuti ndiyomwe ili m’boma and boma lake likungofuna kukawa amphawi ukufunsa chani apa

  46. Nanga zasiyana bwanji ndi ma card a nthawi ya Kamuzu a 50t? heheee! MULULIRANJI?MULULIRANJI LERO UJA MMAKANA KAMUZU

  47. Chiphaso chikasowa u need to pay for replacement osati renewal chiphaso chaunzika sapaka renewal ngati driving license kapena passport musatibere tilikale ndi ululu waumphawi please government

    1. Baba am in south Africa ID iribe expire date go ask Mozambique pple that’s total lie even my girl friend is a south African I don’t see any expire date on her ID zokuba zimenezo trust me mboba

    2. Its only temporary ID if iri ndi expire date ukamakapanga lost ID its when u pay R150 coz u lost it but osataya there is no renewal zankhutu zimenezo

    3. NDE ndati ndizakuba trust me they need njira zibera anthu osauka kukama ng’ombo yoonda kale kumene ID iribe expire date simple

    4. Steve ndelemani bro ndumvetsa zomwe ukamba that is y I said the government just want to steal from poor pple but honestly National ID iribe expiry date akadangoti makadi kapena misonkho ibwelere simple as that but here in South African and all other countries their national ID’s alibe ma expiry date uwu ndi umbava chabe

  48. tiyeni Nazo uko izi!chilichonse chochitika ziko muno cha slow,kukonza magesi kuti asamazimezime mpaka zaka 40,ID yomwe ndaidikira mpaka kutopa!4stek!!!

  49. Zamisala Zokha Zokha Pa Zambia Pomwepa Amapanga Renew Nthawi Imene Amapanga Kalembera Wa Zisankho Okhawo Amene Zimatayika Kapena Alibe Cachgate Basi Ku Mental Ku Zomba Kukudikirani

  50. kkkkk koma amalawi tinadzoloweladi zaulele basi chilichonse kumangofuna kupangilidwa zaulele kwasala mudzaliuza boma lizakugulileni ma tructor kuti izikakulimilani munda mwanu

    1. Kuno ku jozi ndi zimene amapanga nyumba amapatsidwa zaulele,social grant ndi zina zotero but thy still protest and vandalise government properties nde inu mukuti cha ulemu unakupwetekani a Malawi thts why alot of pple amati a Malawi ndugona

  51. Am in abroad I lost my passport and I can’t come to have your I’d that will expire.and I will not be a foreigner if I will come back to stay in my homeland. I got my school certificates from maneb.those are my IDs .because they.don’t expire

    1. kumaika ma comment ngati awa zimangoonesera poyera kuti kumalawi umbuli suzatha … anthu ophunzira koma mbuli … we call them educated savages …..

      how can you say that ur ID its the certificates uve got?? … clearly it doesnt make sense….. !!! id its id … it cant be a certificate …

    2. Koma ,pepani pepani .marilowa ndi obwera .anthu akuja ali ndi ma certificate aku kamuzu accadamy does it mean ndi dzika za malawai .penapake amalawi tidzigani poyankha .

    3. Even Ma Burundi Ali Ndi Za Maneb But That Does Not Mean Ndi Nzika Komanso Iweyo Ukanakhala Kut Ma Id Ako Amaneb Ndiwokhoza Bwino Sibwenz Uli Kumavutoko Koma Zangowonetsa Kupelewera Kwanu Man

    4. Koma iwe overseas yake yiti yosungira mbuli ngati iwe?U r even failing to know hw to differenciate btn academical qualifications and Citizenship,Go back to school bro b4 it z 2late

    5. Oscar kaunda inu ndiye dolo inuyo muli ndichani pamoyo wanu chokuonesa udolo wanu or utakhala ndi ma I D 5 auzika wakowo koma ine sizingandikhuze or ndilibe ID koma ndiine dzika yamalawi

    6. @kamuzu academy u register your nationality even in universities
      So that they can recognized u better with your education credentials if u are qualified for that college . so like me true son of Malawi my school certificates are my IDs of republic of Nyasaland.

    7. And my witineses are my classmates and my teachers and recordings concerning my home village those I registered in schools where I was learning including my relatives and my passport #, that I got from immigration has got my information. Including my relatives too ndiye wina azandimange azabwerese umboni wake woti ndine foreigner

    1. #shaab pita uko munazolowera ku honga anthu obweranu asilamu sika ndiya ulere koma inu mmagula ndemukakanike ku gula ID.koma ainiyakeo sagula tisakunveso ukukomenta mfundoless zakozo.ukuona ngat uli jozi ndi wekha?

  52. Mukuiwala umwini wanu chiphaso ndichofunika chilindi masiku a expire osiyana chifukwa mukamalembetsa zaka zobadwa sikuti nonse munabadwa chaka.chofanana.

    1. ID iribe expire date bodza leni leni I don’t agree with that but only ikatayika u pay some little money simple as that that’s not passport or driving license

    2. Kalembera wa uzika umachitika 10 years iliyose ndiye musakhale mbuli mdziko lanu lomwe
      Kuyambira kalekale
      Moti chaka chamawa kuli kalembera sesasi. Nyumba ndinyumba

  53. Zamasiku omaliza.Olo tidane nazo,palibe chomwe chizasinthe.Palibe ndimmodzi yemwe amene angazakwanilise zofuna za aliyense paekha-paekha.Yense wamaso-mphenya angotsekula maso nkumayang’ana kutsogolo.

  54. Ine ndine mmalawi tsopano mwati unzika umenewu uzikhala ndi expire date meaning kuti u citizenship umenewu ndi wa china2 inu mukuwona bwanji pamenepa.

  55. uwu nde umbamva ndithuuu, kufuna kumabera anthu ovutika kale zoona?? nde ndibwino zingothatu..ma expiry date amaikidwa zaka zosiyana chifukwa chani? kujambulitsa week imodzi koma ena akusiya kugwira ntchito 2023, 2026, 2021 etc…Jesus come back again b4 these thieves succeed with their plans..

    1. Sizingatheke,ndamva kale mu Gulliver mu kuti Chakwera wapanga makadi,fodya weniweni.Kodi mukuganiza kuti south ingavomele zimenezo?

    1. Koma ndiye makona onse ndimaziwa ndikuthana ndi a police osati patrolling akuno Ku jonz wati mor akwathu akachaso aja kkkkkklkl

    2. kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhhkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk id yachani ngati ndirindi passport basi pamenepo tathana

    1. Bodzatu ilo citizenship document iribe expire date but you only pay some little money ukataya.That’s not driving license or either passport baba

Comments are closed.