Timasulileni Baraba – zikutelo nyerere ndi maule

Advertisement
Kamuzu Stadium

Akuti iwo saimva ndipo ngati bungwe la FAM lingapitilize kuwakhomelela, iwo zida ndi zosula kale kuti athane ndi anyamata a Nyamilandu.

Masapota okwiya otsatila matimu a Wandilazi ndi Buletsi aopseza kuti iwo achita zionetselo ngati bungwe loyang’anila za mpira wa miyendo mdziko muno la FAM lipitilize kukaniza bwalo la za masewelo la Kamuzu.

Bungwe la FAM mu sabatayi linalengeza kuti bwalo la za masewelo la Kamuzu silikukwanila kuti paseweledwe mpira. Iwo anati kapinga wonyengezela amene ali pa bwaloli wapelepeseka ndipo pa chifukwa chimenecho sialola kuti matimu azithibulilana pamenepo.

Ganizo la FAM lasiya pa umasiye matimu a mu mzinda wa Blantyre, maka a Bullets ndi Wandalazi amene amadalila bwaloli.

Ndipo pokwiya ndi Nkhaniyi, otsatila matimu amenewa amene amatchuka kuti nyerere komanso ma Pale, iwo ati achita zionetselo kusonyeza kusakondwa kwawo ndi Nkhaniyi.

“A FAM avomeleza ma bwalo e a osalongosoka, ndiye akakanize Kamuzu. Angofunatu aishoshe amenewa,” anatelo mmodzi mwa otsatila Bullets.

Naye mkulu wina wa nyerere anathililapo mang’ombe pochenjeza bungwe la FAM kuti lisiye kuyesa zida.

“Ife ndi nkhalakale za mpira pa Malawi pano. Asamatipute chifukwa atha kupeza mavuto.”

Advertisement

One Comment

  1. Zopusa basi, bwanji nthawi yonseyi simumanga ma stadium anu? Inu ndimasapota Bullets koma zinazi FAM ikuchita bwino. Tinawonjeza.

Comments are closed.